*TONSE ALLIANCE IYAMBA KUKWANILITSA MALONJEZO

olemba Dr Mwale

Kuti ndi DPP ichoke muboma ndi kamba ka manifesto ya boma la Tonse yomwe inatenga mitima ya  anthu ambiri kuphatikizapo achinyamata ndi okalamba.

Mwa Zina Tonse alliance inati izayamba kudula msonkho  pa ndalama zoposera k100,000 ndipo Malingana ndi Avant zikonetsa kuti tsopano malonjezowa ayamba kukwaniritsitdwa pomwe bill imeneyi tsopano yavomerezedwa ndi aphungu mnyumba yamalamulo ndipo kuti ziyambe zikungodikira president chakwera kuti asainire. Koma Malingana ndi mareport aku parliament ndondomeko Imeneyi ikuyenera kuyamba mwezi wa mawa chifukwa mwezi uno watha kalendipo ndondomeko yamalipiro inachitika kele.(avant itsimikizabe ngati zitheke mwezi uno)

Lonjezo lina ndi lokhuza zipangizo za ulimi zotsika mtengo zomwe pakadali pano Avant ingatsimikize kuti zayamba kuchitika mmadera ena pomwe anthu akugula fetereza pa mtengo wa 4499 monga mwa lonjezo.

Inde zokoma zili apo koma achinyamata omwe akusowa zochita ndipo akudalira masewero a mlosera a betting adandaula ndi kukhazikitsidwa kwa msonkho wa 20% izi Avant yapeza kuti zikuthandauza kuti aliyense owina ndalama zoposera 100,000 azidulidwa 20% pa ndalama yapamwamba yo koma ukawina zosaposera 100,000 siuzidulidwa kalikonse Malingana ndi 100,000 tax free.

Bill ya 100,000 tax free ipangitsa kuti ndalama zionjezekere ku salary ya anthu  mdziko muno ndipo izi zibweretsa kutukuka pa chuma. Mwachisanzo ngati umalandira 100,000 ndipo amakudula msonkho wa 10,000 ndipo mu account mwako mmafika 90,000 pano mu account mwako muzifika 100,000 yonse pa mwezi.

Kumbukirani kuti chilichonse chili ndi kuipa kwake apa ogulitsa zinthu nawo akweza mtengo ya zinthu zomwe sizikhala zabwino ayi.

Werengenai zambiri pa www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *