TIKUDIKIRA ATHU OMWE ANAPITA KU MWEZI LERO

Gulu la anthu lotchedwa altemis ll linanyamuka pa 1 April kupita ku mwamba komwe iwo amati akukaona mwezi.
Anthuwa ananyamuka pa dziko pano pa 1 April cha mma 5 koloko mazulo, ndipo zinawatengera masiku asanu ndi limodzi kuti akafike ku mwezi ko,

Pa 1 ndi 2 April akuti iwo anali mudera lomwe amalitcha kuti earth orbit kapena kuti anali akadali mu earth kapena kuti dziko la pansi, ndipo iwo a akhala akuonaona chombo chawo kuti chili bwino bwino? Kuona ma engeen onse kuti atha kukafika ku mwamba komwe kuli mwezi, apatu anali akuzungulira dziko mmwambamo Sikuti anangoima.

Tsiku lachitatu ndi lachinayi anthuwa anali akuyenda kupita ku mwezi, nokha mutha kuona kuti unali ulendo wautali bwanji.
Kenako tsiku la number 5 analowa dera lotchedwa lunar sphere influence komwe akuti mphamvu za earth kapena kuti dziko la pansi zimathera, kumeneko mphamvu imakula ndi ya mwezi, uku akuti kuli mphamvu ija amati gravitational force, ya mwezi.
Tsiku la number 6 anthuwa sopano ndi pamene amauluka mozungulira mwezi komwe amatora zinthunzi zonse zomwe tikuona, atamaliza zonse kumeneko tsiku la number 7 pomwe so ndi pa 7 April anthuwa anayamba ulendo obwera pa dziko la pansi pano.

Anthuwa sanasike chombo chawo ndipo mwezi sanaugunde ayi komwe iwo amauluka ndi komwe kunali mwezi panali potalikirana ma kilomita 6, 545 mukhoza kuona nokha kuti mwina kuchoka ku Nsanje kufika ku chitipa ndi 1, 158 km pomwe anthu anali pa mtunda wa 6 545 kuti akafike pomwe Pali mwezi (Malawi yu ka 6 and half) imagine,

Anthuwa combo chawo anachipanga kuti chizikhala ndi mpweya omwe chimapanga chokha mkatimo, moti amapuma bwino bwino,

Tikunena pano anthuwa atsala pang’ono kuti afike nthawi ikamati 5 :07 pm kwawo kwa azungu pomwe kwathu kuno ndi 8:07 pm

Anthuwa akuti akafikira mu nyanja ya pacific ocean komwe akuti ma boat, sitima komanso ndege zapita kale kukawachingamila
Kenako atengedwa ku bwerera kwawo komwe akalankhula kwa atolankhani,
Kufikira mmadzi ku anapanga dala kuti chombo chawo chisaonongeke pofika pa nthaka yolimba choncho chimafunika pofewa monga mmadzi. Zonsezi ndi zochita kukonza

Avant publications

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *