ANTHU OMWE ANAPITA KU MWEZI ABWERAKO BWINO BWINO

NASA, ndi yosangala kulengeza kuti kwa nthawi yoyamba kuchokera mu chaka cha 1972 pomwe appolo anapita ku mwezi lero anthu ena anayi abwerako ku mwezi atakhalako masiku khumi.

Monga momwe analengezera kuti anthuwa afika 8:07 izi zachitikadi ndendende mu nthawi ya ku dziko lomwe anthuwa afikira. Momwe amafika nkuti ku nyanja ya pacific kukuwala dzuwa ndithu.

Angakhale anthuwa anakumana ndi mavuto ochepa koma izi sizinasokoneze ulendo wawo kapena kubweretsa vuto lililonse ayi.

Anthu onse anayi afika ndi moyo ndipo onse athanzi.
Chombo chimathamanga kwambiri ndipo mmene chimayandikira nkuti ndege zikuuluka kuwadikirira, ma boti okwana asanu ndi limodzi omwe ananyamula athu okwana 41 Anali akuwadikilira.

Chombo Chitafika mmadzi sichinamire ayi koma kuyandama, ndipo zinatenga mphindi zokwana makumi awiri kuti chizimitsidwe ma engeen onse, mwambo owachotsa mu chombo chi watenga pafupifupi 1 hr 34 minutes

Atawatulutsa mu chombo anthuwa anawakhazika pa kena kake (floating boat) komwe anthuwa anakonza pomwe amangoyandamapo ndipo ndege inabwera kuza watenga kukawa Siya mu sitima yomwe imawadikiranso pamodzi ndi anthu oposera 500 mmenemo kuti awalandire.

Ulendowu watenga masiku 9, 1 hr, 32 minus and 15 seconds

Ichi ndi chiyambi chabe chokonzekera ulendo Wina omwe iliko mu chaka cha 2028 pomwe akuti anthu ena apita so ndipo iwo akatsika mu chombo chawo kukayenda kumweziko.

Ndifokokoze kuti enanu munaona mmene chombo chija chimanyamuka ndipo chinali chachikulu komanso chachitali koma Chitafika mmalele chinagawanikana, poti akuti chonse chijavsichikanatha kumafika ku mwezi. chomwe chinagawanikana chija chinatsala mwamba mmomo ndipo sichizabwereranso pansi pano akuti kamba ka force of gravity chizingiloyandama kumeneko ndi ma engeen ake, olo mafuta atatha koma sichingagwenso ayi,

mmawa wabwino

Avant publications

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *