olemba DR MWALE
Nyumba ya malamulo ikadali mkati mwa zokambirana zawo za Chaka Chino ndi mwa Zina anadutsitsa budget yoyamba ya boma la Tonse.
Nkhani yaikulu yomwe inali ku paliyamenti ndi ya 50 + 1 pa chisankho Cha aphungu komanso ma khansala. Mkulu wa bungwe la MEC a chifundo kachali pamodzi ndi MEC yonse analengeza kuti aphungu nawo azigwilitsa ntchito lamulori kuyambira chisankho Cha chibwereza chomwe chichitike pa 10 November 2020 Cha aphungu ndi ma khansala.
Koma aphungu onse mnyumba ya malamulo akana lamulori ponena kuti 50+1 izichitika kwa president yekha basi pakuti amalamula dziko lonse ndipo amapanga ziganizo zikuluzikuku, ndipo kutero izi zitha kuonongetsa ndalama zambiri chifukwa Madera ambiri kumakhala mpikisano kwambiri pakati pa aphungu ndi ma khansala.
Zosangala ndi zakuti avant yapeza kuti aphungu aboma ndi otsutsa onse anavotera kuti pasakhale 50+ 1 pa zisankho za aphungu ndi ma khansala.
Izi zikuthandauza kuti chisankho Cha pa 10 November yemwe watsogola ndi yemwe wapamba basi .
www.avantmalawi.com