SITOLO ZA CHIPIKU ZIYAMBA KULANDILA CHITETEZO CHA ULERE

olemba DR MWALE

Chipiku Sikampani ya boma ayi koma ndi ya anthu (private) ndipo palibe ubale wina uli onse ndi boma ,iwo ali ndi azilonda awo, koma monga mwa chikhalire munthu ukafuna kupanga hayala apolice kuti akapereke chitetezo umayenera kulipira ndalama ya zida za apolice monga mfuti komanso kulipira wapolice yemwe akuzagwira ntchitoyo.

Pakadali pano apolice akudandaula kamba koti tsopano akapita kukagwira ntchito ku chipiku sazilipidwa zomwe zikuthandauza kuti azikagwira ntchito mwa ulere komanso zida za police zizikangogwilitsidwa ntchito ulere.izizikutsatira kulamulidwa komwe kwabwera kuti apolice azitero, koma Avant publications ndi yodabwa kuti Kodi walamula ndani? Nanga cholinga chake ndi chani?
Zikuonetsa kuti kulikulu alipo yemwe ali pa mgwilizano ndi eni ake amasitolowa ndipo pakadali pano sizikudziwika kuti wachita izi ndani koma apolice ayamba kukana kupita kukagwira ntchito mwaulere ku ma sitolo achipiku.

Sitikudziwa ngati nduna yoona za mdziko a Richard Chimwendo Banda aziwa za izi ndipo ngati aziwa ndikhulupira kuti afufuza bwino komanso awuza mthundu wa amalawi chifukwa chomwe achitira izi.

Chenjezo ndi lakuti musaiwale chifukwa chimene anthu anakhala akuyendera mmisewu kwa Chaka chathunthu kufuna kuti DPP ichoke mulowe inuyo. Anthuwatu anafika potopa ndi DPP ndipo zifukwa zake zinali zakatangale ngati zomwezi ,

Musaiwale mwachangu kuti anthu amafika potopa. Iloleni police ikhale yoima payokha wina asalowererepo ayi.

www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *