Ndizachidziwikire kuti a Martha Chizuma anayitanidwa ndi Malawi Police Service ku Area 30 lero nthawi ya 10 koloko mmawa kuti akawafunse mafunso pa uthenga umene unajambulidwa pomwe iwo ankalankhulana ndi chigoba chotchedwa Olama Namalomba. Izi zalemphereka pamene a Malawi ambiri anaonetsa kusakhutira ndikuyitanidwaku ndipo anawopyseza kupanga mademo ku office ya Police.
Muchikalata chimene a Police atulutsa ati iwo ayimitsa kaye mkumanowu kuti apereke mpata kwa a Malawi kumvetsetsa kafukufuku amene a Malawi Police Service amafuna apange.
Nkhani yomwe yautsa mapiri pachigwa ndiyakuti a martha chizuma akufufuza mulandu wa Zanet sattar yemwe wazunguza Malawi yense pa nkhani za katangale ndipo aliyense olimbana ndi nkhaniyi amayenera awone zokhoma basi.
Ngati mkulu wa ACB amalumbira kuzagwira ntchito yake bwino opanda kutulutsa nkhani za bungweri kunja. A martha chizuma monga munthu nawo ali ndi anthu omwe amacheza nawo ndipo amatha kumasukirana nawo mu zina. Miyezi ingapo yapitayi munthu wina yemwe avant publications yapeza kuti amaziwika ndi dzina loti orama Namalomba Koma dzina lake lenieni ndi Anderson mwakyelu ndipo amagwira ntchito ku Accountant General.
Amalawi ambiri ali tcheru pa nkhaniyi kuti amve cheni cheni chimene apolisiwa akufuna kudziwa makamaka potengera kuti nkhaniyi inatha kale kamba koti a president pa 24 january 2022 anaitanitsa a martha chizuma kukawafunsa mafunso pankhajiyi ndipo anawachenjeza kuti izi zisazachitikenso. Ndipo mukulankhula kwawo a president anati ngati anthu ena amafuna kuti martha achotsedwe ntchito kamba ka nkhaniyi nde kuti alemba mmadzi chifukwa munthu aliyense ali ndi zofooka ndipo angathe kukonza ngati ena amuunika choncho a martha nawo atha kuchita bwino pa ntchito yawo kutengera ndi chidzudzulo chomwe alandila. Anatero president wa dziko linoyu. Nalo bungwe la PAC inavomerezana ndi a president pachiganizo chawo choti martha asamuchotse ntchito
Tipite mtsogolo, pano pano patha miyezi itatu pomwe nkhaniyi inachitikira ndipo pakatipa taona munthu wina yemwe dzina lake ndi ashok Nair akutengera martha ku bwalo la milandu kamba ka nkhani ya audio yomweyi. Kamba koti anapaysidwa belo pomwe sizimayenera kutero kba koti anapalamula mulandu waukulu. Koma polisi yathu kunali zii osachitapo kalikonse mpaka anthu anapanga zionetsero.
Amalawi ambiri ali ndi mafunso kuti kodi a polisi anali kuti nthawi yonseyi kuti ayamba kafukufuku wawo? Sabata yathayi zamveka kuti bungwe la ACB lamaliza kafukufuku wake pa nkhani za mulandu wa sattar ndipo akuku akulu ambiri a boma kuyambira 2014 akukhudzidwa ndi katangaleyu ndipo ACB iliyokonzeka kuwatengera anthuwa ku mabwalo amilandu.
Kungotero nthawi yomweyo amalawi awona Bon kalindo watulukira kuchokera kothandiza anthu omwe anavutika ndi ngozi ya madzi ku Chikwawa akuwauza amalawi kuti martha chizuma atule pansi udindo ndipo kupanda kutero achita zionetsero. Kufufuza chifukwa chimwe walakwitsa martha Mumasiku amenewa sichikudziwika, kenaka kuzangomva apolisi akumufuna martha ku area 30.
Kodi chenicheni chomwe walakwa martha ndi chani? Kodi polisi ikutsutsana ndi ganizo la a president? Kodi a Boni kalindo ali mbali yofuna kuthetsa katangale kapena ayi? Nanga ndichifukwa chani akulimbana ndi kuchotsa Martha pa mpando?
Anthu ambiri Ali Tcheru kufuna kudziwa chimene Malawi Police Service ikufuna kumva kwa a Chizuma amene potengera kuti a president ndi PAC anakamba kale nkhaniyi inatha.
Kodi kapena apolisi akufuna kukadziwa yemwe a chizuma amalankhulana naye? Nanga kutenga nthawi konseku amadikira chani. Kodi yemwe amalankhulana ndi martha anamutuma ndani chifukwa kumapeto kwa audio yawo asanadule foni kukumveka munthuyo akuuza mzake kuti umu ndi mmene ndimalankhulirana ndi martha.
Anthu ena Ali ndi mafunso kuti a Namalomba dzina lawo ndi ndani? Ife a avantmalawi timawadziwa a Namalomba ndi dzina lawo leni leni ngati Anderson Mwakyelu amene amagwira ntchito ngati ku Accountant General komabe amazizimbayitsa pamene Ali ndi ma reporter ena ku America omwe amalowaso pa page yawo
Funso likupweteketsa mmutu mkumati, kodi iwowa sayitanidwa ndi a police? Nanga kodi iwowa anawatuma ndani kujambula lamya imene amkalankhula ndi a Chizuma? Kodi a Chizuma anawakhulupirira bwanji a Namalomba kumakamba nkhani zochuluka?
Mafunsowa Ali chonchi, tiyeni tizukute Police Service yathu ku Malawi imene yadya wani Pankhani za chinyengo zokhudzana ndi Sattar.
Kodi a Police wa akugwira ntchito mmalo mwa a Malawi? Kodi iwowa akuyimira lamulo la dziko la Malawi? Kapena a police wa Ali pansi pofuna kutseka pakamwa a Chizuma kuti asawafufuze pa zachinyengo zomwe amachita?
Zambiri tsatirani avantmalawi.com ndi ine
DR MWALE