APOLISI AKUSAKA A KALIYOPA

Mkulu wina amene akudziwika ndi dzina loti Chipiliro Kaliyopa akufunidwa ndi a Police pamene analandira ndalama kwa achinyamata powalonjeza ntchito ku Malawi Police.

Mkuluyu pakulankhula dzana ndi atolankhani analonjeza kuti akazipereka mmanja mwa a Police lachitatu, Koma mpaka pano mkuluyi sanakazipereke kupolisi ndipo mkuluyi akuthawathawa.

Mu mawu ake kaliyopa anavomera kuti iwo analandira K37,000 kwa achinyamata oposera 50 ngati transport yopititira ku Kanjedza ku Blantyre kukaphunzira za Police.

Koma lero pakulankhula ndi mneneri wa Police a Harry Namwaza watsimikiza kuti mkuluyi akuthawathawa. Ndipo akufuna kwabwino adziwitse a Police za komwe kuli Mkuluyi.

Kunamiza anthu powabera ndalama ndi mulandu waukulu ndipo munthu umayenera kugamulidwa kukakhala kundende ukapezedwa olakwa.

Ma report omwe avant publications yalandira akuti angakhale mkuluyi akukana kuti sanalandire ndalama zokwana 150,000 kwa achinyamata aliyense, ena mwa omwe anapereka ndalamazi abwera poyera kuti iwo anawauza kuti anene izi powaopsyeza, ndipo pakadali pano atha kuulura zonse kamba koti ndi owawidwa mtima.
Nawo makolo a anyamatawa omwe ambiri amachokera boma la Lilongwe akhumudwa pomva kuti mkuluyi akukana kuti sanalandire ndalamazi. Ndipo iwo akuti kaliyopa afufuzidwe komanso amangidwe posatengera chipani chimene amachokera.

M’modzi mwa anyamatawo wati umboni okwanira pankhaniyi ndi ma foni omwe iwo amalumikizana naye ndipo atha kukatenga zonse zomwe amakambirana nawo kampani ya ma foni a m’manja ngati angapitilize kukana za nkhaniyi.

Zambiri tsatani pa

AVANT MALAWI.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *