CHIHANA APANIKIZIKA PARLIAMENT

Olemba DR MWALE

Phungu wa kumpoto kwa boma la mzimba a yeremiya chihana anauza nyumba ya malamulo kuti ali ndi umboni oti boma la Tonse likuchita zachinyezo ndipo iye ali ndi umboni omwe ukuonesa kuti bomali linalandira ndalama mwachinyengo mu ma ulamuliro wawo womwe wayamba kumenewu ndipo iye akuziwa komwe ndalamazi zili.

Atalankhula izi sipikala wa nyumba ya malamulo analamula a chihana kuti apereke umboni pa nkhaniyi kufikira dzulo pa 10 September koma achihana sanapereke umboniwu.

Naye chakwera dzulo anauza a chihana kuti akwere limodzi convoy ya apresident ndikupita komwe iye akuti kuli ndalama koma akalephera anthu aziwe kuti chihana ndi waboza.

Lero mtsogoleri wa nyumbayi a Richard chimwendo Banda anauza a speaker kuti a chihana apereke umboni zomwe speaker anachitadi koma chihana analephera kupereka umboni ponena kuti malamulo sakutero koma speaker anapanikiza phunguyi koma zachisoni walephera kutero ndipo iye walonjeza kuti abweretsa ma documents ake 2  koloko masana ano ku office ya speaker. Aphungu amukuwiza chihana chifukwa cholephera kukhala ndi umboni pa zomwe akhala akunena.

Speaker wati ngati chihana sapereka umboni masana ano ndekuti alandira chilango pa mchitidwe wakewu.

Onani zambiri pa www.avantmalawi.com

Share this article

One thought on “CHIHANA APANIKIZIKA PARLIAMENT

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *