olemba DR MWALE
Boma la Tonse lapereka budget yake ku nyumba ya malamulo yomwe Malingana ndi a mlusu ikukwana 2.190 trillion.
Ndalama za misonkho yomwe amalawife timapeleka komanso zomwe tapatsidwa ndi Maiko akunja zonse zakwana K1.435 trillion
Ndalama zomwe amalawi amadula ziphaso zakwana K 1.179 trillion
Ndalama zachitukuko zomwe zagwilitsidwa ntchito ndi K 511.6 billion
A mulusu ati ndalama za misonkho zomwe boma limatorera zatsika ndi 11.% munyengo ya covid19 ndipo boma lawo ligwira ntchito ndi bungwe lotorera misonkho(MRA) kuti liyambe kutoreranso ndalama zokwanira.
Boma la Tonse lalengeza mu budget yake kuti ndalama zodulidwa mtsonkho tsopano zakwera kuchoka pa 45000 kufika pa 100,000 kusonyeza kuti ngati budget imeneyi idutse nde kuti izi ziyambika.
Poti mu budget yongogwilizira ya K722 billion anangozikamba koma amadikira budget yaikuluyi.
Msulu wauza nyumba ya malamulo kuti boma lawo limanga bwalo la zamasewero la azimayi (netball court) yamakono mdziko muno komanso limanga mzuzu youth center yomwe boma la DPP lakhala likulonjeza koma osachita.
Pankhaniyi ya zomangamanga yomweyi ndunayi yati boma la Tonse limanga misewu iyi:
kasungu -mzimba M1 road, Jenda – Embangweni road, Njakwa Livingstonina road komanso Thyolo – bangula road mwazina.
Nkhani yomwe www.avantmalawi.com amalawi akhala akudikirira ija tsopona yafika magetsi ndi madzi kulumikiza mwa ulere, a mulusu akuti ndi khumbo la boma kuti anthu ake apeze madzi ndi magetsi mosavuta koma izi tsopano zidikira nduya yoona ma re-form a Dr chilima omwenso ndi a vice president a dziko lino kuti amalizitse mbali yawo ndi mabungwe awiriwa (escom ndi waterboard)
Nawo anthu a khungu la chi albino boma lawaganizira powapatsa ndalama zokwana K400 million
Boma la Tonse lathetsa ndondomeko ya IMF (international monitory fund) komanso (ECF) (Extended Credit Facility) kuyambira lero. www.avantmalawi.com
Boma la Tonse lisintha dzina la bungwe lopereka ngongole lomwe limachedwa kuti MEDEF ndipo iwo alipatsa dzina lina ,pakadali pano boma likupanga Kaye kafukufuku wa mmene ndalama zinayendera ku MEDEF.