BURGET IKUYENDA MOTERE

Olemba DR MWALE

*BUDGET YA CHAKA CHA 2020-2021*

Boma la Tonse lapereka budget yake ku nyumba ya malamulo yomwe Malingana ndi a mlusu ikukwana *2.190 trillion.*

Ndalama za misonkho  yomwe  amalawife timapeleka komanso zomwe tapatsidwa ndi Maiko akunja zonse zakwana *K1.435 trillion*

Ndalama zomwe amalawi amadula ziphaso zakwana  *K 1.179 trillion*

Ndalama zachitukuko zomwe zagwilitsidwa ntchito ndi *K 511.6 billion*

A mulusu ati ndalama za misonkho zomwe boma limatorera zatsika ndi 11.% munyengo ya covid19 ndipo boma lawo ligwira ntchito ndi bungwe lotorera misonkho(MRA) kuti liyambe kutoreranso ndalama zokwanira.

Boma la Tonse lalengeza mu budget yake kuti ndalama zodulidwa mtsonkho tsopano  zakwera kuchoka pa 45000 kufika pa 100,000 kusonyeza kuti ngati budget imeneyi idutse nde kuti izi ziyambika.
Poti mu budget yongogwilizira ya K722 billion anangozikamba koma amadikira budget yaikuluyi.

Msulu wauza nyumba ya malamulo kuti boma lawo limanga bwalo la zamasewero la azimayi (netball court) yamakono mdziko muno  komanso limanga mzuzu youth center yomwe boma la DPP lakhala likulonjeza koma osachita.

Pankhaniyi ya zomangamanga yomweyi ndunayi yati boma la Tonse limanga misewu iyi:

kasungu -mzimba M1 road,  Jenda – Embangweni road, Njakwa Livingstonina road komanso Thyolo – bangula road mwazina.

Nkhani yomwe www.avantmalawi.com amalawi akhala akudikirira ija tsopona yafika magetsi ndi madzi kulumikiza mwa ulere, a mulusu akuti ndi khumbo la boma kuti anthu ake apeze madzi ndi  magetsi mosavuta  koma izi tsopano zidikira nduya yoona ma re-form a Dr chilima omwenso ndi a vice president a dziko lino kuti  amalizitse mbali yawo ndi mabungwe awiriwa (escom ndi waterboard)

Nawo anthu a khungu la chi albino boma lawaganizira powapatsa ndalama zokwana *K400 million*

Boma la Tonse lathetsa ndondomeko ya IMF (international monitory fund) komanso (ECF) (Extended Credit Facility) kuyambira lero. www.avantmalawi.com

Boma la Tonse lisintha dzina la bungwe lopereka ngongole lomwe limachedwa kuti MEDEF ndipo iwo alipatsa dzina lina ,pakadali pano boma likupanga Kaye kafukufuku wa  mmene ndalama zinayendera ku MEDEF.

Boma la Tonse lati likweza malipiro a anthu ogwira ntchito m’boma ndi 42%

Alimi okwana 4.2 million ndi omwe apindure ndi fetereza otchipa koma kusiyana kwake ndi kwakuti fetereza sayendera koponi ayi koma aliyense amene ali ndi chiphaso cha unzika.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *