THE MATTER IS IN COURT
Mlandu wa mtsogoleri wa chipani cha UTM ulowa mu court lero pomwe ma jaji akuyembekezeka kupereka chigamulo pa mulandu oti a chilima analandila ndalama kuchokera kwa a zunnett Satter.
Lero bwalo silitenga nthawi kwambiri kamba koti ndikungopereka chigamulo pa zomwe boma likuchita pa mlanduwu.
A mbali ya a chilima komanso bwalo la milandu linalamula a mbali ya boma komanso nthambi yachitetezo ya MDF kuti ipereke zikalata zomwe zikuonetsa yemwe anasainira mgwiriizano wa sattar ku MDF koma boma pamodzi ndi MDF onse akukana kupereka zikalatazi ponena kuti muli maina a anthu ena omwe sakufunika kuti atchulidwe komanso zitha kusokoneza zinthu Zina.
Pachifukwa ichi bwalo lero likuyembekezeka kugamula kuti Bola lalephera kupereka umboni nde lionenso kuti mlandu ulipo kapena palibe.
Mlanduwu ndi umene upereke chitsogozo chonse pa mgwlizano wa Tonse. Ndipo amalawi ambiri akuyembekezeera kumva mawu a Dr Chilima pamapeto a mlandu.
Avant publications sikusiyani nonkha ndipo ikupatsirani tsatanitsatani wa nkhayi.
DR MWALE