MILANDU YONSE IWERUZIDWE PASANATHE MASIKU 90

Mkulu wa mabwalo a milandu a chief just Rezin mzikamanda wauza ma jaji ake onse mdziko muno kuti apereke zigamulo zamilandu yonse pasanathe miyezi itatu.

Dziko la Malawi lili ndi mabwalo a milandu ambiri ndipo ma jiji nawo ndi ochuluka kutengera kuti president wa dziko lino waonjezeranso oweruza ena mumabwalomu. Komatu chodabwa ndi chakuti milandu yambiri ikadali mu khoti ndipo zigamulo sizinaperekedwe.

A mzikamanda ati ndizomvetsa chisoni kuti pali anthu ena onwe ali kundende kudikira chiweruzo koma ma jaji kapena kuti otengera milandu ku khoti sakupanga izi. Tikudziwa ndi otanganidwa koma asamaiwale kuti anthu ena ali ku ndende pazifukwa zomwe sizikuyenera kuti akhale kumeneko ndipo ufulu wawo uli mmanja mwa ma jajiwa choncho ndikuuza mabwalo onse mdziko muno komanso ma jaji onse kuti aliyense awonetsetse kuti milandu yomwe ali nayo ifike kumapezo pakutha pa miyezi itatu.

Sitikudziwa ngati ngati zimene anena mkulu wa mabwalozi zikuthandauza milandu yonse angakhale yakatangale ya anthu andale yomwe ikungogonera mumabwalo milandu.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *