MATSE ALOWA MMANDA LERO

Dziko la Malawi ndi lachisoni pomwe lero likukaperekedza oyimba otchuka Martin nkhata aka matse yemwe anamwalira dzana kamba kopsya ndi moto.

Monga avant publications inanenera mwambowu uyendetsedwa ndi boma ndipo tikunena pano anthu ayamba kale kusonkhan pa civo stadium mu mzinda wa lilongwe. Oyimba ambiri, amipingo, andale komanso magulu a anthu osiyana siyana omwe amakonda katswiriyu akukhamukira kumaloku kukapereka ulemu omaliza kwa namandwayu.

Dziko la Malawi Lataya mnyamata wa luso ndipo mbiri yake sizafufutidwa mdziko muno.
Pakadali pano avant publications ikuuza mtundu wa amalawi kuti tipewe kufalitsa nkhani za bodza pa infa ya mnyamatayu ndipo aliyense atenge zomwe akubanja anene ponena kuti kufalitsa nkhani za bodza kukhoza kupitiliza kuswa mitima ya anamali zomwe zingayambitse mapokoso.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *