John Zenus Ungapake Tembo anabadwa pa 14th September Mchaka cha 1932 M’boma la Ntcheu ku Kasinje kumene Bambo ake a Zenus Ungapake Tembo anali M’busa wa Mpingo wa Church of Central African Presbyterian pa Khola CCAP nthawi imeneyo. A tembo kwawo kweni kwenikweni ndi ku Dedza.
Monga Mwana M’busa, John Zenus Ungapake Tembo anali Mwana owopa Chauta, Ndipo Iye atamaliza Maphunziro ake a primary anasankhidwa kukapitiliza Maphunziro ake pa Blantyre Secondary School (BSS) ndipo atamaliza Maphunziro ake a Secondary Iye anapita ku Dziko la Lesotho komwe anakapitiliza Maphunziro ake pa Sukulu ya Ukachenjede yotchedwa University of Roma.
John Tembo akuphunzira pa Sukulu ya Ukachenjede ya Roma, M’dziko la Lesotho, kumeneko anadyelera Maso kwa Namwali wina Dzina lake Ruth yemwe anadzamanga naye Banja patsogolo.
Ndipo Mchaka cha 1958, John Tembo anapeza Bachelor of Arts in political Philosophy.
Atabwelera ku Malawi, John Tembo anayamba ntchito ya uphunzitsi pa Dedza Secondary School komwe anaphunzitsa kwa Zaka ziwiri ndipo anadzatumizidwa ku Sukulu ya secondary ya Robert Blake M’boma la Dowa komwe anakapitiliza ntchito yake ya uphunzitsi.
Mchaka cha 1960, Patangotha Zaka ziwiri Kamuzu Banda atabwera ku Malawi, John Tembo anayitadwa kukhala Phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Dela Lakum’mwera M’boma la Dedza.
Apatu nkuti Dziko la Malawi lisanalandire ufulu odzilamulira ndipo Mchaka cha 1964, Dziko la Malawi Litalandira ufulu odzilamulira, John Tembo anasankhidwa kukhala Nduna ya Zachuma mu 1964 mpaka 1969.
Kumbukirani kuti paja John Tembo anali ndi Bachelor’s Degree ya Political Philosophy ndipo Munthu yemwe anali oyenera kukhala Nduna ya Zachuma anali Dunduzu Chisiza, Koma Iye anamwalira pa Ngozi ya Galimoto.
Pa nthawi ya Chipwilikiti ndi Chifwilimbwiti cha Nduna za Boma, Mchaka cha 1964( Cabinet Crisis) John Tembo sanatule pansi udindo wake wa Nduna monga momwe Nduna zina zinachitira.
A Tembo anakhalapo Gavanala wa Bank yayikulu mu dziko muno lotchedwa Reserve Bank. Komanso chairman wa Blantyre print.
Wolemekezeka a Tembo adakhalapo wotanthauzira chizungu mu chichewa Dr Hastings Kamuzu Banda akamalankhula ku mtundu wa a Malawi.
A John Tembo adayimiraponso Chipani cha MCP pa zisankho za President mu zaka za 2004 ndi 2009 ndipo adagonja kwa mtsogoleri wakale wa dziko lino professor Bingu wa Mutharika.
Titha kutsimikiza kuti Chipani cha MCP chitatuluka m’boma Dr Tembo anachisunga kwa za ka zoposera makumi awiri akuchiramulira.
A Tembo adakwatira mzimayi otchedwa Ruth, ndipo asiya ana asanu mwa ena ndi Chimwemwe Dudu, John Tembo Jnr, Thambo Themba ndi Dalitso Tembo.
Mzimu wa a Tembo uwuse mu mtendere.
Tsatani Avantmalawi.com
Deeply concerned hence the only God who given us has also snatched out of us ,may his soul rest in everlasting piece