Mahomed Hannif adathawa atagwilira mtsikana wazaka 14

“`Apolisi apereka chilolezo chomanga a Mahomed Hannif, wazaka 56 waku Pakistani omwe akuimbidwa mlandu wogwiririra mtsikana wazaka 14.

Hannif akumuganizira kuti adagwiririra mwanayu mu Marichi chaka chatha ku Mudi ku Blantyre.

Malinga ndi lipoti la Malawi Police, Malawi Human Rights Commission komanso Center for Human Rights Education, Advice and Assistance, a Hannif anali akuimbidwa mlandu wokhudza kugwilira komanso katangale koma adatathawa kuzengedwa mlandu.

Mabungwe atatuwa apempha omwe akudziwa komwe Hannif ali kuti akawonekere kupolisi yapafupi.

“Tikufunanso kuchenjeza anthu onse kuti ngati aliyense atapezeka kuti akuthandiza wothawayo m’njira iliyonse adzakumana ndi milandu,” akuwerenga gawo la chikalatacho.“`

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *