ZAGWA ZATHA
Taonani chithunzicho. Anali limodzi ku khoti anthuwa. Patsala mmodzi.
Dziko la Malawi likudutsa munyengo yoipa kwambiri pomwe nsanamila imodzi ya ndale yathyoka. A chilima lero kulibe, zonsezi ndi chifunga.
Zagwa zatha poti madzi akataika saoleka. pomwe ngati dziko tikhale tikulira imfa ya a chilima kwa Matsiku makumi awiri ndi limodzi 21, ndikoyenera kuti ntchito zisaime, moyo upitilire. Nazo ndale sizingaime ayi.
Chipani chomwe chakhudzidwa kwambiri pa ndale ndi chipani cha UTM, pomwe yemwe anali mtsogoleri wawo ndi yewemwe wachoka pakati pawo. Ena amati chipanichi anthu samachikonda koma amakonda a chilima, ndipo kuchoka a chilima chipaniso chatha. Kodi mawu awa apherezera?
Diso la ndale likuona patali zomwe zichitike mu nyengo imeneyi. Kodi atenge utsogoleri wa chipanichi ndi ndani tsopano? Inde kukamba za nkhaniyi lero ndikufulumira kwambiri, koma poti masiku amatha ndi kugona, chisankho nacho chayandikira ndipo zonse zikufunika ku chitika mwachangu.
UTM ikadali mugwilizano ndi chipani cha MCP chomwe chinalengeza kale kuti mtsogoleri wawo Chakwera azaimanso 2025, izitu zinalengezedwa a chilima akadali moyo. Lero mkulu uja watisiya kodi mugwilizano ukhala po? Diso la ndale likuyang’ana mwachidwi zomwe zichitike masiku akudzawa. Kodi ku UTM atsogolere ndi ndani? Malingana ndi ndondomeko Zimakhala zachidziwikire kuti oyamba akachoka Wachiwiri atenge malo ake, choncho mmene achoka a chilima, Dr machael Usi amayenera atenge udindowu koma anthu ambiri ataya chikhukupiliro mwa a Usi popeza ati Sama onetsa chidwi chokhala limodzi ndi anzawo munyengo ya mulandu wa achilima kukhoti komanso ndi omwe amayenera kutsogolera anzawo pa msonkhano ya atola nkhani munyengiloyi koma iwo samatero. A Usi anapangitsa msonkhano wa gulu lawo la odya zake alibe mulandu komwe kunalibe makaka a chipani cha UTM, izitu zimachitika a chilima ali moyo kodi pano pomwe a chilima amwalira a Michael Usi amubayabe kunsana chilima angakhale ali mmanda?
Mphekesera zikumveka kuti a masangwi ndi omwe atenge udindo wa a chilima, koma kunena zoona a masangwi si otchuka kwambiri mchipanichi kuposa anthu ena, poti munthu chimakutchukitsa ndi chipani monga anachitila achakwera, chilichonse ndi chotheka, koma funso nkumati ali ndi mfundo? Akopa achinyamata? Diso la ndale likungoona zonsezi.
Mphekesera ina ikuti a kweni atsogolera chipanichi. Pamenepa diso la ndale likuonapo chani? A kweni ali ndi chikoka ndipo ndi odziwika mdziko muno, mayankhulidwe awo ndi achikoka kwa achinyamata, azimayi komanso azibambo, a kweni ndale achitapo ndipo akhalapo Nduna zosiyana siyana. Kodi at awapatsa chinthuchi a kweni apitilize zomwe a chilima amafuna? Koma anthu ena a madana ndi ulamuliro wa azimayi, kodi atapatsidwa mwayi a kweni zingatani?
Mpungwepungwe tsopano uli kwa mtsogoleri Chakwera pomwe akuyembekezeka kusakha Wachiwiri wake mmatdikub7 akubwerawa. Bomali ndi losonkherana, oyamba anachoka ku MCP ndiwo achakwerawa ndipo Wachiwiri anali a chilima, ndizachidziwikire kuti Wachiwiri akuyenera kuchoka ku chipani cha UTM,
Kodi achakwera aphangira zonse kupereka ku mcp? Kodi akatero apereka uthenga otani kwa anzawo omwe ali nawo mugwilizano? Kodi akaperekera mpandowu ku UTM apereka uthenga otani kwa anzawowa? Alangizi a Chakwera gwirani ntchito yanu bwino apa muunikireni mtsogoleri, motobunayaka kale nyumba ikupsya iyi. Muzimitsa kapena muonjezera petulo?
Ambiri otsatila chipani cha UTM sakumvetsa ndi zomwe zachitikazi ndipo iwo akuti chipani chawo chituluke mu mugwilizano. Koma ndi ovuta popeza zomwe a maganiza achilima sizikudziwika. Ndi chifukwa chake anthu Ena akuti adikire mayi chilima popeza ndiwo akudziwa zambiri. Koma dziwa I kuti ndale zaku mtundu sizabwino. Ndi so la ndale likutero.
Imfa ya achilima yazetsa zokambakamba zambiri mdziko lino kamba koti izi zachitika kwa munthu yemwe amafunika kuzapikisana nawo pa chisankho chikubwerachi. Imfa iyi kunena zoona yawachotsera chikoka achakwera komanso chipani cha MCP. Nkutheka chipanichi sichikukhudzidwa nkomwe pa zomwe zinachitikazi koma poti ndi ndale mbiri ya chipanichi yada basi. Wina afune asafune apa mavoti ena a mcp achotseredwa,
Amalawi sachedwa kuyiwala taonani anthu ayamba kupasa molaro adadi.
Ena nkumafunsa kuti pa maliro ndi chifukwa chani a Chakwera sanalankhule posanzikana ndi achilima dzulo? Diso la ndale linaona kale kuti izi sizichitka kamba ka zomwe zinachitika ku Bingu stadium lamulungu. Ngati achakwera amakuwidwa pa kwawo kuli bwanji ku Ntcheu? Ichi ndi chifukwa chake panalibe wa ndale mmodzi yemwe a anayankhula posafuna kubweretsa chisokonezo.
Malawi ali pa Mpungwepungwe kwambiri pa ndale.
Akulu akulu a chipani cha UTM ati sapota weni weni wa chilima sangasiye chipani poti chilima wamwalira koma iwo ati aliyense wa UTM achilimika pofuna kukwanilitsa khumbokhumbo la achilima.
Zachitika mdziko muno ndi phunziro kwa atsogoleri athu kuti asamale pochita zinthu kamba koti za mawa siziziwika, koma mukati muone ndi diso la ndale mugwilizano uja unali wa zipani ndipo mmapepala zilipo. Kodi mugwilizano upitilira kapena ayi?
Avant publications
DR MWALE