BISHOP MSUSA ALANKHULA MOMANGA MALAWI

Bishop Thomas Luke Msusa ati mulungu anali ku Chikangawa mmene zonse zimachitika ndipo sanamizika.

Iwo ati anamufunsa mulungu kuti ndi chifukwa chiyani walora izi. Iwo anati mulungu adawayankha kuti simudandifunse pamene ndinalora mwana wanga Yesu Christu kufa imfa yowawa. Iwo ati mulungu akufuna kuonetsa ukulu wake.

Mwambo wa msembe ya Misa uli mkati ndipo ngati mphatso yapadera Bishop Thomas Luke Msusa wapereka mwambi oti ” Chitsime chikaphwa ndipamene kuya kwake kumaoneka”.

Archbishop Thomas Luke Msusa alangiza anthu kuti ngati akusungira miyala yogendera anthu, apite akagwiritse ntchito ngati mafuwa pophikira nsima, ndipo ngati ali ndi zikwanje akadulire mitengo osati kukhapira ena.

A Msusa amema anthu kulira mwa Mtendere chifukwa Saulos Chilima anali munthu wa Mtemdere. Iwo ati sikwabwino kuti a Chilima ayikidwa kuli ma phokoso chifukwa izi sizipereka chithunzi thunzi chabwino ku Malawi.

Archbishop Msusa wati malirowa ndiopweteka ndipo wati ngakhale afiti nawo akumva kuwawa mmalo moti mwina azikondwera.

Msusa wati Chilima wafela mbendera ngati momwe analosela.

Avant Publications

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *