CHAKWERA KULANKHULA PA REPORT LA ACB

Pa 21 June chakwera walankhula ku mtundu wa amalawi pa zomwe zili mu report lomwe ACB yakhala ikufufuza zokhuzana ndi katangale.

Chakwera wapeza mfundo zingapo zomwe zamukhuza mu report limeneri ndipo sanabise chichewa koma kuzuzula polakwika komanso kupanga chiganizo chake.

Kwa zaka 4 nthambi za police ndi ya asilikali akhala akupereke ma kotintirakiti 16 ku ma kampani okwana asanu omwe onse ndi a satter ndipo ndalama zake ndizoposera 150 million dollars, zomwe malingana ndi chakwera ati sizikuyenera kukhala choncho ndipo mchitidwe uwu usinthidwe.

A chakwera ati malingana ndi report la ACB nthawi zambiri komanso zopweteka ndi zoti boma limagulitsidwa zinthu modula kwambiri, ndipo katundu oti amagulilitsidwa pa 2000 dollars a satter amagulitsa pa 1.7million dollars zomwe. Ndi ndalamazochuluka kwambiri. Chopweteka kwambiri ndichakuti public procument office imadziwa za izi koma imalekerera mwadala osafufuza zomwe zaonongetsa ndalama za amalawi zochuluka.

Ndipo anthu ena ogwira ntchito muboma monga oyimira boma pa milandu awiri opuma (sanatchulidwe maina) anapereka chilolezo kuti sattar sakulakwitsa ndipo atha kumapanga ma business ake, izitu zimachitika mwa dala podziwa zoti nawo amadyera mmomo.

Lipoti la ACB likuonetsa kuti pali anthu okwana 53 omwe analandila ndalama kwa sattar kuchokera mu March 2021 ndi October 2021. Apatu ndikuti tonse alliance yalowa kale mu boma.

Anthu ambiri omwe akutchulidwa mu report ndi ogwira ntchito ku nthambi za boma monga, police. Army, MRA, MBC, ku finance, reserve bank, homeland affairs, tourism, state house, ma khoti komanso angakhale ku bungwe lomwero lofufuza za katangale, ACB. Ndipo anthuwa tikawaphatikiza akukwa 84. Koma chodabwitsa kwambiri bungwe la ACB lakana kuulula maina a anthuwa. Funso nkumati akubisa chani ngati afufuza zenizeni?

President chakwera wati malingana ndi lipoti limeneri mu kabineti yake mulibe yemwe watchulidwa kupatula a Chilima. Koma pa maina amenewa 84 pali anthu ena okwana 13 ndi omwe bungwe la ACB lafufuza kotheratu kuti anapangadi za katangale.

Chakwera sanakhale chete atamva za izi ndipo iye wapanga chiganizo chake Pa anthu angapo omwe akugwira ntchito mu nthambi za boma zomwe iye ali ndi mphamvu kupereka chigamulo pa iwo ndi zili motere.

Anthuwa ndi mkulu wa polisi a George kainja, iwowatu bungwe la ACB lili ndi umboni onse pa zomwe analankhulana ndi sattar kuti apange ma dilu awo. Apa bungwe la ACB silikufunanso umboni wina popeza zonse amachita kukambirana zikumveka bwino bwino. Pachifukwa ichi achakwera ati mkulu wa polisiyu wachotsedwa pa udindo wake.

Prince kaponda mgaga yemwe ndi oyang’anira nyumba ya chifumu ayimitsidwa kaye pa ntchito yawo mpaka afufuzidwe kaye. Komanso mkulu wa bungwe la public procurement naye yemwe amayenera kulondoloza za katangale waimitsidwa pa ntchito yake.

Achilima sanaimitsidwe kamba koti achakwera alibe mphamvu zochotsa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu popeza naye anachita kusankhidwa ndi anthu. Koma zomwe wachita chakwera ndikusiya kuwatuma a chilima pa ntchito zina zonse za boma. Mpaka ACB ipereke zenizeni zomwe chilima anachita.

Angakhale chakwera wapanga chiganizo ichi koma iye wauza mtundu wa amalawi komanso bungwe la ACB kuti angakhale akapondamgaga, mkulu wa bungwe la Public procurement atchulidwa palibe chomwe bungweri lafotokoza kuti anachita. Nawo vice president a dziko lilo angotchulidwa koma palibe chomwe akunena kuti achita. Funso la chakwera ku ACB ndi loti kodi anthuwa apalamula chani? Nanga akutchulidwa kuti atani? Malingana ndi chakwera iye wati bungwe la ACB lasowa chilungamo pa nkhaniyi chifukwa angotchula anthu opanda zolakwika zomwe zingathe kubweretsa chisokonezo.

Iye wapanga chiganizo chowaimitsa anthu enawa pa ntchito zawo kamba kongotchulidwa, report la ACB silikupereka chilichonse pa nkhani za chilima. kusiyana ndi a kainja omwe zifukwa zawo ndi zomveka chifukwa pali umboni.

ACB sinaitanitse a kaponda mgaga ndi anzawo komanso a chilima kukawafunsa mafunso. Nde zakatangalezi amapanga motani? Kunena zoona ndimaona ngati achilima anapanga zoipa monga mmmene lipoti linali masabata atatu apitawo koma kuwerenga report ili silikupereka chilimbikitso pa nkhaniyi kamba koti ilibe umboni watero chakwera.
Apa ndikupempha bungwe la ACB kuti lizikhala siliyasi pa ntchito yawo chifukwa apa zikuonetsa kusagwira ntchito kwawo mosayenera zomwe zingachotse chikhulupiliro cha anthu mwa iwo.

Chakwera waonetsa kukhumudwa kwake ndi bungwe la ACB chifukwa zinthu zingapo sizinafufuzidwe bwino. Bungweli lati anthu anayamba kulandila ndalama kwa sattar mu chaka cha 2008 ndipo bungweri lili ndi maina ake koma zonsezi mu report ili mulibe. Chakwera wadabwa kuti iye anapempha ACB kuti ipereke liport la katangale pa nkhani ya sattar koma mmalo mopereka maina onse ACB yapereka maina oyambira mu 2018 okha, apa chakwera akuti bungweri laonetsa kukondera popeza likuchita kusankha anthu owatchula mu lipoti limeneri.

Ripotili lati sattar wakhala akuperekanso ndalama ku zipani za ndale mu nyengo ya kampeni zomwe iye wavomerezana ndi a martha chizuma kuti andale aziulula ndalama zomwe ali nazo kusiyana ndi kusaulula chifukwa zimapangitsa zipani kupanga ziphuphu, apa chakwera wati zipani zonse zifufuzidwe.

Malingana ndi lipoti la ACB zikuonetsa kuti bungweri lakondera pakupereka lipoti lake zomwe chakwera wazuzula poyera, anthu onse ochokera 2008 bwanji sanatchulidwe? Ndi munthu mmodzi yekha yemwe ali ndi umboni kuti anachita izi. Ndipo ndi a kainja okha, Kodi ntchito muzigwira choncho? Nde a kaponda mgaga ayimitsidwa chifukwa chani? Achilima alakwa chani kutchulidwa?

Chakwera wakhumudwa ndi ACB popereka ripoti ku Parliament komanso ku mabwalo a milandu ponena kuti ngati anthuwa alandira riport ndichimodzimodzi kuti amalawi onse aziwenso.

Izi ndi zomwe zachitika mdziko muno

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *