AWOTCHEDWA NDI MOTO

A Zuze Tama yemwe akuti anali m’modzi wa anthu opanga zauchifwamba aotchedwa ndi moto mpaka kufa mbom la Nsanje. Izi zachitika kumbandakucha kwa lero m’mudzi mwa mfumu Nsambakaluma TA Chimombo.

Anthu ena auza www.avantmalawi.com kuti anthu okwiya anatentha mkuluyu chifukwa chovulaza modetsa nkhawa a Emanuel omwe amapanga malonda wobwerekesa ndalama komanso kunyamula anthu ndi katundu pa Kabaza.

Pakadali pano www.avantmalawi.com yauzidwa kuti a Emanuel atengeredwa ku chipatala ndi apolisi omwe anabwera pa malowa a Zuze Tama ataphedwa kale.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *