ATATU AMWALIRA PANGOZI YA KU MCHINJI

Anthu atatu amwalira pamenenso ena avulala modetsa nkhawa galimoto yomwe anakwera itasempha mseu wa M12 ndikugudubuzika kangapo pafupi ndi mudzi wa Chiphala ku Mchinji.

Mmodzi wa anthu wopulumuka pangoziyi, a Mathews Chatambalala ati ngoziyi yachitika pafupi ndi mlatho wa Bua pomwe Iwo anali paulendo wopita ku Namitete m’boma la Lilongwe komwe kunali mwambo wa maliro a wachibale.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’boma la Mchinji, a Limbani Mpinganjira, galimotoyi yomwe ndi ya mtundu wa Double cabin, Nissan Hard body, nambala BQ 1023, inanyamula anthu 14 paulendowu.

AMpinganjira ati galimotoyi inachita ngozi dalaivala yemwe ndi Christopher Siliya atalephera kuongolera bwino atafika pamalo angoziwa.

Mkulu woyang’anira zaumoyo m’boma la Mchinji Dr Yohane Mwale ati mzimayi wa zaka 62, Jennifer Banda komanso Collins Manfred Ngoma anamwalilira pamalo angoziwa pamene mmodzi wamwalira atangofika naye kuchipatala chachikulu Cha Kamuzu Central komwe anamutumiza.

Pangoziyi, dalaivala wagalimotoyi ndi ena ovulala pang’ono awagoneka pa chipatala Cha Mchinji.

(By Dumisani Mwambazi-Mchinji)
Avantmalawi.com
25/03/24

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *