AWATHIRA UTSI WOKHETSA MISOZI

Apolisi ku ku City centre mu mzinda wa Lilongwe athira utsi okhetsa misozi kwa achinyamata omwe anaima mu msewu pofuna kuonetsa kukhumudwa ndi kuchedwa kwa ulendo wawo opita kukagwira ntchito m’minda ya mdziko la Israel.

Ena mwa achinyamata omwe ali ndi chiyembekezo chopita kukagwira ntchito mdziko la Israel monga mwapangano la dziko lino ndi dziko la Israel anaima pa mseu wopita ku nyumba yachifumu yadziko lino ku city centre mumzinda wa Lilongwe poonetsa kukhumudwa ndi kuchedwa kwaboma kupereka chilolezo choti anyamuke kupita ku Israel.

Malinga ndi mmodzi wa oimira achinyamatawa, a Thomas Msosa ati Iwo anapanga izi pofuna kuti mtsogoleri wadziko lino awaone komanso amve madandaulo awo chifukwa amayenera kupita ku Israel miyezi ingapo yapitayi koma boma likuchedwa kupereka chilolezo choti Iwo anyamuke.

Achinyamatawa anaima mumseu ngakhale kuti bwana mkubwa wa boma la Lilongwe anawaletsa kutero kamba koti amati adikire lachiwiri pomwe magulu okhuzidwa adzakumane.

Achinyamatawa ati iwo sadamvere zomwe bwana mkubwayu ananena kamba koti amafuna mtsogoleri wadziko lino awaone pamene azidutsa mumsewu pomwe akupita ku Dowa masanawa.

Iwo ati kuchedwa kupita ku Israel kukupangitsa kuti azikhala moyo wovutika kamba koti anatenga ngongole komanso kugulitsa katundu wawo pokonzekera za ulendowu.

(By Dumisani Mwambazi-Mchinji)
avantmalawi.com

25/03/24

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *