Mtsogoleri wa chipani chotsutsa yemwenso ndi pulezidenti wachipanichi a Peter Munthalika asintha malo a aphungu awo mu nyumba ya malamulo.
Malingana ndi chikalata chomwe avant publications yaona chikuonetsa kuti mtsogoleri wa chipanichi munyumbayi a kondwani nankhumwa achotsedwa pa malo awo omwe amakhala ndipo tsopani iwo apatsidwa mpando wa chisanu ndi chiwiri (7) ndipo malo awo tsopano apatsidwa kwa phungu wa kumwera cha ku zambwe kwa mulanje a George Chaponda. Malingana ndi malamulo mtsogoleri wotsutsa m’nyumbayi amayenera azikhala pakati osati komwe amusunthiraku.
A Kondwani Nankhumwa omwe ati chikalatacho sichinawapeze awonetsa kudabwa ndi nkhaniyi ponena kuti izi ndi zachilendo mu mbiri ya demokalase.
Mtsogoleri wa Otsutsa mnyumbayi a Kondwani Nankhumwa anasintha makhalidwe a phungu m’nyumbayi posachedwapa zomwe zimapangitsa a shadreck Namalomba
Kukatenga chiletso chomwe chaletsa kusinthaku ndipo a muthalika atengera mwayi pa chiletsochi kuchotsa a nankhumwa pa malo awo omwe amakhala.
Ngakhale izi zili Choncho, Chief whip Hon Chiponda ati iwo akudabwa kuti malamulo a Parliament amapereka mphamvu kwa mtsogoleri otsutsa boma yekha kusintha makhalidwe mu Parliament, kotero tsogoleri wa chipani sakuyenera kutero
Mpungwepungwe unakapitilirabe mchipani cha DPP pomwe ena akufuna nankhumwa kuti atsogolere chipani ndipo ena sakufuna, pakadali pano sitikudziwa ngati a nankhumwa awachotsa pa mpandowu kapena ayi kutengera ndikusinthaku.
www.avantmalawi.com
DR MWALE