Chigulu cha anthu olusa amenya ndikupheratu mfumu kadzabwa omwe amachokera mwa a gurupu a Chathasa mfumu yaikulu kachere ku Dedza kamba kopha mwana.
Chatsitsa zaye ku njovu ithoke mnyanga nchakuti mmudzimo munachitika malilo Sabata yatha ndipo zinamveka kuti anamwalirayo anagwa mu ntengo ndipo anthu anakhulupirira. Koma patapita matsiku ana anzake anayamba kuulula kuti mzawoyo sanagwe muntengo koma anachita kuphedwa ndi amfumuwo ndikumutayira muchitsime. Izi zinakwiyitsa anthu a mudzimo omwe anakhamukira kunyumba kwa amfumuwo kukawapanikiza ndi mafunso ndipo anavomera za nkhaniyi. Anawa anaulula kuti mkuluyi anatilonjeza kuti tisaulure ndipo atipasa K100 aliyense koma tikapita kolonjerera akuluwa samatipatsa ndalama zathu
Apa anthuwo anayamba kumenya mfumuyi kuti iwulule zambiri ndipo inaululadi kuti anthu ambiri omwe akhala akufa mmudzimo amawapha ndiyeyo ndipo anatchula maina awo, zomwe zinapangitsa anthu kukwiya kwambiri mpaka kupha amfumuwo komanso kuotcha nyumba zawo.
Chodabwitsa ndichakuti mmene nyumbayo imapsya mnyumbamo mmatuluka anthu omwe samadziwika ndipo anali ambiri komanso mmene amachokera pamalopo samadziwikanso
Pano apolisi atenga onse okhudzidwa ndi imfa ya mwanayo
www.avantmalawi.com
DR MWALE