A DAUSI ALOWA MCP.

Phungu wa dera lapakati m’boma la Mwanza a Nicholas Dausi lero abwerera ku chipani cha MCP atachotsedwa ku chipani cha DPP.

Hon Nicholas Dausi, phungu wa dera la pakati pa boma la Mwanza ati ndi bwino kumakhala bwino ndi anthu.

Kotero iwo amayika Chitukuko pa tsogolo kusiyana ndi ndale. “Ndinachotsedwa ku DPP chifukwa chopempha chitukuko ku boma zimene sizili zofunika pa democracy. Mwana akasochera amayang’ana kumene wachokera, ndichifukwa ndawona kuti chitukuko chikhalepo kwathu kuno ndibwerere ku MCP.”

Iwo ayankhula izi pa nsonkhano wachitukuko omwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera akuchititsa m’boma la Mwanza.

M’kuyankhula kwawo iwo anati pa nthawi yomwe amachoka m’chipani cha MCP, m’chaka cha 2007, akuti adanenetsa kuti sadzanyoza atsogoleri a chipanichi.

A Dausi atiso akadakhala kuti amanyoza akuluakulu a chipani cha MCP pa nthawi yomwe anali ku DPP, a Chakwera sakadabwera ku dera kwawo ndikukhazikitsako ntchito za chitukuko.

Izi zachitika patangodutsa masiku ochepa chabe, akuluakulu a chipani cha DPP atachotsa Dausi ndi anthu ena, mchipanichi.

AVANT Publications

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *