Yemwe amatsogolera zionesero za malawi sali bwino mdziko muno a Bon Kalindo ati ayamba ayimitsa kale zionesero zonse zomwe anakonza.
Poyankhula ndi atolankhani mumzinda wa Lilongwe a Kalindo ati ayamba ayimitsa kaye zioneserozi pofuna kupatsa mpata boma kuti liyambe lakonza kaye madandu omwe iwo anawapatsa mmbuyomu.
Iwo ati chiganizochi chabwera kamba koti awona kuti boma la Tonse motsogozedwa ndi a Chakwera akuonetsa chidwi ndikuyankha zomwe iwo akhala akunena.
Akalindo ati boma linamva ndikutsitsa mitengo ya ma tolgate, komanso kuchotsa nduna yakale ya za malo a Kezzie Msukwa kamba ka nkhani za katangale.
Akalindo ati kuimisa zioneserozi kwazanso pofuna kupereka mpata ku boma kuti lithane ndi mavuto angozi za kusefukira kwa madzi komwe kwakhuza anthu ambiri mchigawo chakumwera. Koma akalindo sananene kuti zioneserozi zizayambiranso kapena ayi.
Kuimitsa kwa zioneserozi kwadza mkatikati moti mkuluyi akuyankha milandu Itatu yomwe anamangidwa pazifukwa zosiyanasiyana.
www.avantmalawi.com
DR MWALE