Kuli Chitetezo chokhwima ku Mzinda wa Mzuzu pamene kuli zisankho zosankha tsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM)
Zisankhozi zikuchitikira ku Sunbird Mzuzu Hotel kumene a Fleetwood Haiya akupikisana ndi a Walter Nyamilandu Manda pa mpando wa President wa FAM. Komatu Kumaloku kukhalenso kuvotera komiti yayikulu ya akuluakulu oyendetsa mpira ku Malawi kuno, ngakhale zili choncho, komabe tikuona mpando umene watsitsa dzaye ndi wa President wa FAM.

A Walter Nyamilandu Manda akhala pa mpandowu kwa zaka 19 ndipo iwo akufunitsitsa atavoteredwa kuti apitilize ntchito ku FAM, pamene a Fleetwood Haiya akhala pa mpando kwa zaka zisanu ku SuperLeague of Malawi (SULOM) imene imayendetsa mipira ija ya TNM, ndipo iwo akufunitsitsa atakhala president wa FAM kuti asithe kayendetsedwe ka mpira.
Koma kwa amene tafika ku Mzuzu titha kutsimikiza kuti ulendo wofika ku Sunbird Hotel, ndi chimodzi modzi ulendo okafika ku Blantyre chifukwa cha kuchuluka a polisi komanso asilikali mu Nseu.

Avant Publications ikhale ikukupatsirani tsatane tsatane wa zochitikazi, ndipo mukhala ndi ine #Vinjeru Ngwira