UTM CONVENTION

Tikulandireni kuno ku chigawo cha kumpoto makamaka mu mzinda wa mzuzu komwe chipani cha UTM chikhale chikusankha atsogoleri ake atsopano omwe ayendetse chipanichi zaka zisanu zikubwerazi. Chipani cha UTM kwa nthawi yoyamba chichititsa msonkhano wake wa ukulu ku chigawo cha ku mpoto. Mu mbiri ya dziko lino aka ndi koyamba kuona chipani chomwe chili ndi owatsatila ambiri kuchititsa msonkhano ngati uwu ku mpoto, kamba koti zipani zina zimachititsa msonkhano wawo ku chigawo chomwe zikuchokera ndipo chipani cha aford chomwe chimachokera ku mpoto chimachititsa msonkhano wake ku chigawo cha pakati.
A UTM achiona cha nzere kuchititsa msonkhanowu ku kuchigawo chomwe mtsogoleri wawo Anamwalilira.

Zokonzekera zonse zili Mchimake ku Mzuzu pa Chisanga Complex, imene yayang’anizana ndi Mzuzu University.

Mipando 60 ndimene ikuyenera kuvoteredwa ndipo ma delegates 800 ndi amene akuyembekezera kuponya Voti yawo. Avant publications itsindike pano kuti atsogoleri onse omwe a kupikisana nawo pampando wa u president anafika dzulo ku mzuzu ndi owatsatila awo.

Dr Michael Usi amene ali President wachipanichi sapezeka nawo pa mwambowu umenewo, malingana ndi a Usi, iwo akuti oyendetsa mwambowu sanatsate malamulo a chipanichi kotero kuti sangakhale nawo mugulu la anthu ophwanya malamulo. Izi sopano zikuthandauza kuti mlembi wa mkulu wa chipanichi ndi yemwe atsegulire ndi kutseka msonkhanowu.

Uku kukhale koyamba mu mbiri ya dziko lino kuona mtsogoleri wa chipani akukana kukhala nawo ku msonkhano wa ukulu wa chipani chake. Mmbuyomu taona Zipani zina atsogoleri awo anakhala nawo pa ma Convention amene achitika. Izi zikuzetsa nkhawa kwa anthu kuti a Usi Ali ndi malingaliro okasumira chipanichi msonkhanowu ukatha.

Avant publications ikupatsilani zonse mwa tsatanitsatani

Avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *