GWEDEGWEDE KU DPP

Olemba DR MWALE

Mavuto sakutha kuchipani chotsutsa boma Cha DPP makamaka pa nkhani ya omwe akuyenera kutsogolera chipani mnyumba ya malamulo.

Lero kumangochi kunali msonkhano wa akulu akulu achipani Cha DPP  komanso mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mthalika.

Pa msonkhanowu anthuwa agwilizana kuti achotse anthu ena omwe sakutsatira malamulo achipanichi.
Lero DPP yachotsa anthu anayi omwe ndi vice president wachipanichi mchigawo Cha kumwera a Kondwani Nankhumwa, grezelder geffrey,yusufu nthenda komanso a happier mhango.
Malingana ndi a brown mpinganjira akuti anthuwa achotsedwa chifukwa chosatsata www.avantmalawi.com malamulo mu chipanichawo.
Nkhani yomwe yautsa mapiri pachigwa ndi yakuti Kondwani Nankhumwa asakhale mtsogoleri wotsutsa mnyumba ya malamulo koma izi sizinatsangalatse akulu akulu ena omwe akufuna Nankhumwa.

Avantpublications yapeza kuti chipani cha DPP anachiyamba ndi munthu wa kunthyolo ndipo sakufuna wina wa boma lina alamulire apa tikuona Nankhumwa wakumulanje akumukhomerera,

Maudindo omwe analimo anthu omwe achitsedwa apatsidwa www.avantmalawi.com kwa anthu ena motere, a mwanamveka omwe tsopano ndi vice president wakuchigawo Cha kumwera, a Tembenu ndiwo alowa mmalo mwa grezelder geffrey ndipo a nickson masebo alowa mmalo mwa a happie mhango ngati msungi chuma.

Mawa kumayembekezeka kuchitika msonkhano wina waukulu wa DPP koma anthu rna akana kupita kumsonkhanoko kamba ka zomwe akuchita akulu akulu chipanichi.
www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *