Chitatuluka muboma pogonja pachisankho koyamba chipani Cha DPP tsopano chayamba kuika chikhulupiriro chake mwa a Madalitso Kabambe omwe apuma kumene pa ntchito yawo ngati gavanala wa banki yaikuku mdziko muno.
Malingana ndi Avant Publications, akabambe ati akhala akuuzidwapo ndi akulu akulu a DPP kuti Iwo ndi omwe ali oyenera kuzatsogolera chipanichi muchaka Cha 2025. Atafunsidwa maganizo awo akabambe ati nawo monga munthu akuunika Kaye maganizo achipanichi asanavomere.
Udindo wa otsogorera chipani umafuna munthu yemwe ali okhwima munzeru komanso yemwe ndi chuma. Ndipo akabambe ali ndi zoyenera zonse kamba koti Iwo asiya kumene ntchito yawo ku reserve Bank komwe amalandira ndalama zokwana 24 million pa mwezi ngati salary osaphatikizirapo ma alawansi, ndipo Iwo akhala akulandira ndalamazi kwa zaka zitatu ndi theka. Akabambe ati iwo samalandira 27 million monga mmene anthu amanenera ndipo iwo ati palibe chovuta chilichonse kumalandira ndalama yochuluka chotere kamba koti ntchitoyo ndi yaikulu komanso yofunika ukadaulo
Kubwera kwa dzina la akabambe mu chipani Cha DPP kusokoneza khumbo khumbo la Nankhumwa omwe maso awo nawo ali pa mpando wa u president wa chipanichi mu Chaka Cha 2025. Kodi izi zitha bwanji ku DPP?
www.avantmalawi.com
DR MWALE