NORA DOCHERTY FOUNDATION IPEREKA FETEREZA WA ULEELE

Nora Docherty foundation ndi bungwe lomwe linakhazikitsidwa ndi mzungu waku America yemwe dzina lake ndi Nora Docherty iyeyu cholinga chake ndikutukula maphunziro mmalawi muno. Nora anasankha dera lotchedwa chiluzi kudedza kwa mfumu yaikulu kasumbu. Kumeneku mzunguyi wamangako ma school awiri chiluzi ndi chimphandu ndipo ana akumadya phala tsiku lililonse zomwe zapititsa patsogolo maphunziro muderali.

Bungweli linamanganso chipatala ndikupereka ambulance kuti amayi oyembekezera onse asalipire koma kumawatenga ulele kupita kuchipatala nthawi yochira ikakwana.

Pomwe nyengo inkunka navuta pa nkhani ya kudula kwa fetereza bungweli lapereka matumba awiri awiri a fetereza (wanthaka ndi obereketsa) aliyense kwa anthu okwana 1400. Nkhaniyi yadzetsa chimwemwe ku dera la anthu a mmudziwu ndipo ayamika bungweli kamba kochita zosowa ngati izi.

A mfumu achiluzi ati mwayi ngati uwu sunagwerepo mdera lawo ndipo zomwe lachita bungweli ndi mdalitso wapadera.

Nora Docherty mwini wake anamwalira ndipo mwana wake ndi amene akupitiliza zonse zomwe mayi ake anayambitsa.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *