Nduna ya zachitetezo a Richard chimwendo Banda alankhula mawu omwe awusa mtsutso mmalawi muno pomwe awuza mtundu wa amalawi kuti mukapeza munthu wogwililira ameneyo mmenyeni,langani ndipo mthyoleni ndipo akamazafika kupolisi tiziziwa kuti mwachita naye.
A chimwendo alankhula izi kamba koti mchitidwe uwu wawonjeza kwambiri mmalawi muno. Ndipo boma likuyeyesa kupereka zilango koma ndipomwe akukhala ngati akukolezera.
Koma Malingana ndi HRDC yati iwo akudabwa kuti ndunayi ikuuza amalawi kuti azitengera malamulo mmanja mwawo. Kodi munthuyo akamupha boma lizawaimba mlandu omwe apha munthu pomumenya?
Koma malingana ndi owona ufulu wa ana ndi azimayi a Babra Banda wati ndunayi pena pake akuimvetsetsa chifukwa yalankhula izi pokwiya ndipo chiyembekezo chawo ndi choti anthu awopa kuchita izi.
Kodi achimwendo Banda alakwitsa?nanga a HRDC akulakwitsa? Kodi a Babra Banda alankhula bwino poikira kumbuyo ndunayi?
Avant publications ikufuna kumva ndemanga yanu pa khaniyi.
www.avantmalawi.com
DR MWALE