MTSIKANA WAZIPHA KU MWANZA KAMBA KOLANGIZIDWA KUTI AKHALE NDI MAMUNA MODZI

Mtsikana wa zaka 18 ku Mwanza wadzipha atayambana ndi makolo ake atamulangiza zokhala ndi mam’muna mmodzi yekha yemwe akuyembekezereka kukwatirana naye.

Izi zachitika kucha kwa lero kunyumba yamakolo amtsimanayu mmudzi mwa Nchotseni mfumu yaikulu Kanduku m’bomali.

Monalisa Chibowa ati anali ndi chibwezi chomwe chili ku South Africa pa mgwirizano oti adzakwatirana.

Mkati mwa sabatayi , mayi ake anamulangiza zokhala ndi mamuna mmodzi yekha ataona njira zina zomwe amayenda zosakhala bwino ndipo anamuophseza kuti ngati atapitiliza adziwitsa maumunayo.

Kamba ka izi, kamba kokhumudwa , mmawa wa dzulo anamwa mankhwala ochotsa moyo omwe anagwira ntchito kwambiri kucha kwa lero kufikila wafa.

Apolisi anatengera thupi la mtsikanayu ku chipatala cha Mwanza District komwe anakatsimikiza za imfa yakeyi ndipo padakali pano thupi lake likhala likupita kumudzi kwao ku Zomba kukaikidwa mmanda.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *