MKULU WA MANEB ATULE PANSI UDINDO. YATERO HRDC

Kutsatira zomwe zachitika mkatikati mwa mayeso a MSCE bungwe lomenyera ufulu la HRDC lalowererapo ponena kuti mkulu wa maneb ature pansi udindo kamba koti sakumakhala siliyasi ndi ntchito yake ,Avant yapeza kuti mayeso anayamba kupezeka kwa ana olemba mayesowa tsiku lolemba lisanafike ndipo poyamba tinkaona ngati ndizaboza potengera kuti ku MANEB kumakhala chitetezo chokwanira. Koma zachisoni kuti pafupifupi subject iliyonse inaoneredwa ndipo tikunena pano phunziro lomwe amafuna kulemba lero ndi mawa likuzunguliranso mmasamba amchezo.

HRDC yakwiya kuti anawa sanalembe mayeso munthawi yake  kamba ka corona ndipo pomwe amaona kuti tsopano amalaliza maphunziro awo aku sekondale nkhani yachisoni ngati iyi ndikumachitika.

HRDC yati mkulu wa maneb ature pansi udindo wake mmatsiku asanu akubwerawa ndipo akapanda kutero  iwo amema ana onse a secondary kuti ayende mmisewu kuonetsa mkwiyo wawo. (Ngati simuzitenga bwino a maneb zionetserozi zitha kukhala zoopsya chifukwa ana asukulu komanso makolo akwiya)

Nduna ya zamaphunziro inalengeza dzulo kuti mayesowa awaimitsa ndipo akuyenera kuzalembedwanso mu March Chaka Cha mawa. Anyalonje ati anawa sazaperekanso ndalama ya mayeso koma sizikudziwika ngati azaperekenso school fees.

Avant publications ikufuna kuti bungwe la MANEB lifufuzidwe kuti apeze yemwe anatulutsa mayeso chifukwa zachitikazi zapweteketsa wina osalakwa yemwe sanaonereko nkomwe.

Ngati dzulo ku mzuzu,Lilongwe, ntcheu ndi Brantyre ana anayamba kupanga zionetsero paokha nanga HRDC ikalowerera kuzakhala bwanji?

www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *