Ulendo wathu unayamba bwino bwino, kufika mu Lilongwe ku kawonera masewera a mpira pakati pa Silver strikers (ma bankers) ndi Ekwendeni Hammers umene ma bankers atenga Chikho atapambana zigoli ziwiri kwa iyayi.
Komabe mkati Kati mowonera mpira, reporter wa Avant anatsikira ku zimbudzi za Bingu National Stadium kumene anakawona mbonawona. Chinachitika mchakuti mtolankhaniyu atafika kuzimbudzizi analandilidwa ndi fumbi la dothi la katondo wa Mu Lilongwe.
Ndi zoonadi ku Lilongwe mkwa fumbi koma sizimayenera Stadium yomangidwa bwino ngati Bingu kukhala ndi zimbudzi za fumbi losowa poponda.
Izi zinapatsa chidwi mtolankhaniyu pamene anatola zithunzi komanso kulemba chibaluwa kwa oyanganira bwaloli kuti ngati mkotheka aziyesa kukonza, kupukuta komanso kukolopa mu zipindazi kuopa kuzachititsa dziko la Malawi Manyazi kutabwera alendo oyang’anira ngati a CAF ndi Ena.
Zambiri tikupatsirani pa avantmalawi.com