Dr Shepherd Bushiri Agawa Chimanga ku khwimbi la anthu

Prophet Shepherd Bushiri yemwe ndi mtsogoleri wampingo wa Enlightened Christian Gathering(ECG) kapena kuti The Jesus Nation, wagawa chimanga lero kwa anthu omwe akusowa chakudya opitilira 18, 000 mu mzinda wa Lilongwe.

Mwambo wogawa chimangachi unachitikira kulikulu lampingowu ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe.

Anthu ozungulira madera a Kauma, Chilinde, Kawale, Senti, Chimoka, Mtandire komanso ena anafika kumalowa kudzalandira thandizoli.

Mmawu awo, a Bushiri ati ntchito yogawa chimangayi yafikira kale maboma a Mzimba, Karonga, Nkhotakota, Ntcheu, Lilongwe, Rumphi, Mulanje, Thyolo, Zomba, Nsanje komanso Nkhatabay.

Anthu ochuluka alandira chimanga kuchokera kwa Mneneri wa Jesus Nation. Prophet Shepherd Bushiri

Anthu ochuluka mdziko muno akukhudzidwa ndi kusowa kwachakudya kamba kakusowa Kwa mvula komanso namondwe wa Freddy zomwe zinapangitsa anthu kusakolora zakudya zochuluka

(Dumisani Mwambazi-Mchinji)
avantmalawi.com
17/03/24

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *