Boma likuyenera lichitepo kanthu msanga pa matenda a cholera omwe abuka kunkhatabay. Avant publications yachita chidwi kamba kosowa thandizo komanso malo oyenera othandizira odwala, pa chipatala chaching’ono ku tukombo anthu akulandira ma drip a madzi omwe achita kupachikidwa muntengo.
Izi zikuchitika pomwe ndalama za nkhani nkhani zikuonongedwa pa zinthu zomwe sizingapindulire nzika za dziko lino. Boma likufunika kuti liike chidwi pa nkhani za umoyo pomanga zipatala za makono komanso kulemba ntchito ma nurse ochuluka , koma mpaka lero ma nurse omwe anamaliza maphunziro awo 2014 sanalembedwe ntchito pomwe mzipatala ogwira ntchito akuchepa.
Kusowa nthandizo loyenera komanso ogwira ntchito ochepa kunkhataby kupereke phunziro ku boma la tonse kuti lichitepo kanthu msanga pa nkhani za umoyo mdziko muno.
www.avantmalawi.com
DR MWALE