olemba Dr Mwale
Bungwe la chipembedzo Cha chisilamu lomwe likutchedwa kuti Muslim Association of Malawi (MAM) lamanga sukulu ya sekondare kwa Chikuse mfumu yaikulu Kasumbu m’boma la Dedza.
Malingana ndi kafukufuku yemwe Avant publication yapanga , yapeza kuti sukuluyi yamangidwa ndi ndalama zokwana K45 million.
Wamkulu wa bungwe la MAM, a John kazembe wati sukuluyi ichepetsa mtunda omwe ana amayenda kupita ku sekondare yomwe ili pafupi.
Naye khansala waderali anali okondwa kamba ka thandizoli poti ana tsopano achepetsa mtunda womwe amayenda.
Malingana ndi mtola nkhani wathu yemwe wakhala akuyendera derali wati kwa T A kasumbu kuli sukulu zasekondale zitatu zokha zomwe ndi Makota yomwe Ili kwa Kanyama, ina ili kwa kasumbu kwenikweni komanso Mpalare sekondare.
Kumangidwa kwa sekondale ya kwa chikuse kuchepetsa chiwerengero Cha ana omwe amachokera mmadera monga Madzumbi, Mwenje, komanso ena a mbali zaku Mayani koma oyandikana ndi chikuse poti tsopano azitha kusankhidwira komweko.
Dera la chikuse likuonekabe lotsalira mpaka pano koma chonsecho ma basi ankafika kumeneko nthawi ya ulamuliro wa pulezidenti woyamba Kamuzu Banda komanso kunali post post office yodalilika nthawiyo koma chifukwa Cha kulekerera boma linawaiwala malowa.
Pang’ono ndi pang’ono chitukuko chikubwera ku derali kamba koti kunalinso mavuto a network yomwe pano ndi mbiri yakale.
Anthu akuderali akuti ndi okondwa kwambiri kamba ka chitukuko cha sukuluyi koma tsopano pempho lawo ndilakuti boma liwamangire nsewu kamba koti kuderali kumachokera zakudya zosiyanasiyana zomwe amadyetsera boma la Dedza komanso mzinda wa Lilongwe koma mayendwe ndiwo akuvuta.
Ndemanga zanu mutha kutumiza ku
www.avantmalawi.com
DR MWALE