By Dr mwale
Chipani Cha DPP chachotsa mlembi wake wankulu mayi grezelder Geffrey kamba ka mawu ake omwe anayankhula dzulo oti Peter munthalika tsopano apume ntchito yawo agwira. Titalankhula nawo a Grezder Jeffrey atsimikiza kuti zakhala bwino kuti iwo akapume mkuchita ntchito zina
Angakhale zili choncho koma akulu akulu a chipani cha DPP akana kuti nkhaniyi ndi yabodza koma malingana ndi ma report omwe www.avantmalawi.com yapeza akuonetsa kuti mawu omwe analankhula mayiyu akwiyitsa milumuzana ya DPP
Nkhani ngati yomweyi ndi yomwe inapangitsa kuti calister mthalika komanso bonnie Kalindo achotsedwe muchipani Cha DPP.

Pakadali pano nkhani yomwe ikutipeza kumene ikuonetsa kuti a Ben phiri nawo atula pansi udindo wawo muchipanichi ndipo iwo akudikira kuti DPP kudzera mwa Peter munthalika avomereze ganizo lawoli.

Nkhani yavuta ndi yakuti Peter mthalika apume kapena azaimenso?