Chipani Cha MCP chati boma la Tonse lichotsa ogwira ntchito ena ku bungwe lopereka ngongole kwa anthu la NEEF lomwe mmbuyomu limadziwika kuti MERDEF ati kamba koti mwa ena anthuwa ndi achipani Cha DPP omwe akulepheretsa kuti anthu alandire ndalama pofuna kuti amalawi ayambe kudana ndi president chakwera ponena kuti walephera kuwapatsa ngongole anthu.
Polankhula pa mwambo okumbukira malemu kamuzu Banda ku Blantyre a Moses kunkuyu ati ndi zodandaulitsa kuti mmalo moti amalawi alandire ngongole zomwe boma linalonjeza koma anthu ena akukhomerera Ngati ndalamazi ndi zawo. Izi sizikuchitika ku NEEF kokha ayi komanso mu nthambi zina za za boma nde ife takhala tikuona izi ndipo tipereka maina a anthu oterowa kwa mtsogoleri wa dziko ,anatero a Kunkuyu dzulo.
Mawuwa adza pomwe amalawi ambiri akudandaula kuti zofunikira zonse anapanga zoti atenge ngongole koma mpaka pano miyezi isanu yadutsa ndalama osalandila za NEEF, Pomwe nthawi ya season ikutha.
Tsiku ndi tsiku ku ma ofesiwa kukumakhala gulu la anthu otiazapange za ngongole koma palibe chikuchitika, funso kumati ndalama zilipo kapena palibe?
Nawo anthu okhudziwa kulilongwe akufuna kupanga madermo kupita ku ma office a NEEF kuti akawauze chomwe chavuta kuti asalandile ndalama zomwe boma linapereka kale.
www.avantmalawi.com
DR MWALE