OGWIRA NTCHITO KU ESCOM AKUFUNA KUNYANYALA NTCHITO

olemba DR MWALE

Mpungwepungwe wabuka ku bungwe la ESCOM pakati pa ogwira ntchito ndi boma kamba ka ndondomeko ya tsopano yomwe boma likukhazikitsa ku bungwe la ESCOM.

Kudzera mukafukufu yemwe Avant publications yapeza kuzera mwa ogwira ntchito ku ESCOM (omwe sitiwatchula dzina pazifukwa) yapeza kuti mkati mwa ESCOM muli ka bungwe kena kotchedwa single buyer function, avantmalawi komwe tsopano akapanga kuti ndikoima pakokha.bungweli ndi lomwe alipatsa mphamvu zogulitsa magetsi komanso kuyang’anira zonse zokhuza ndalama za magetsi, izi zipangitsa kuti bungwe la ESCOM lisamakhale ndi ndalama ndipo lizichita kugawilidwa ndalama zotsala kuchokera ku single buyers function (SBF). Tikunena pano boma lapanganso kampani ina ku ESCOM konko yochedwa power market limited. Izi zikuthandauza kuti escom ikugawanika.

Ogwira ntchito onse aku ESCOM akutsusana ndi ganizo loti single buyer ichoke mu ESCOM chifukwa iwo akuona kuti ogwira ntchito sanauzidwe bwino kuti ntchito yawo ikhalapo kapena ayi? Kuchotsa SBF mu ESCOM ndekuti ESCOM ikhala yopanda ndalama yolipira anthu ake, komanso izi zapangitsa kuti Magetsi akwera mtengo komanso msonkho ukwera chifukwa ndalama zomwe amalawi akhala akugula magetsi ziziyendetsa ma company atatu omwe ndi ESCOM, single buyers komanso EGENCO.

Ogwira avantmalawi ntchitowa anauzapo nduna yoona za mphamvu za Magetsi za nkhaniyi koma zikuoneka kuti sizikuphura kanthu, anthuwa kudzera mukukambirana kwawo anapereka matsiku 21 kuti boma lisinthe maganizo ake pa nkhaniyi ndipo akapanda kutero ogwira ntchitowa ayamba kunyanya ntchito, yatero kalata yomwe anthuwa alemba ndipo wasaira ndi mlembi wa bungweli a William Mnyamula.

Izi zizapangitsa kuti mmalawi muzakhale opanda Magetsi mpaka nkhaniyi itatha. Ma reforms amenewa analipo kale ndipo tsopano akungokwaniiritsidwa, koma funso nkumati Kodi sizichotsetsa ntchito anthu izi?chimene anthu aku ESCOM akufuna ndi gurantee ya ntchito yawo komanso kuti anthu asapwetekeke polipira ma bill ochuluka ndicholinga choti boma lipeze ndalama zoyendetsera ma company atatu.

Onani zikalatazi.

www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *