Malingana ndi kafukufuku ozama yemwe wachitika ku tukombo m’boma la nkhatabay pa nthenda yomwe inabuka masabata atatu apitawa tsopano zatsimikizika kuti ndi cholera.
Malingana ndi a Director of health and social services a Dr mwatikonda Mbendera, iwo auza avant publications kuti nthendayi inayezedwa koyamba ndipo zotsatira zinaonetsa kuti pali kachilombo kena komwe kamatchedwa kuti e. Coli komwa kamayambitsa zizindikiro zotsekula komanso kusanza zomwe zimafana ndi zizindikiro za cholera koma panthawi sanapeze kuti ndi cholera. Izi zinapangitsa kuti akatswiriwa aunikebe mozama ndipo zotsatira za ma kuyeza komaliza kunaonetseratu poyera kuti tsopano nthendayi ndi cholera. Ndipo achipatala alengeza kuti tsopano mu boma la nkhatabay ku tukombo tsopano kwabuka nthenda ya cholera. A mbendera anafotokoza kuti poti palinso kachikombo ka e coli sanganeneretu kuti nthendayi ndi cholera yokha koma kuti pofuna kuthana naye boma liyesetsa kuthana ndi cholera komanso kachilombo ka e. Coli.
Avant publications inalankhulananso ndi a khansala a mderali a mr Acran Chenya iwo ati ndiokhumudwa kwambiri kuti nthenda yoopsya ngati iyi yabuka mdera lawo ndipo iwo achita chotheka kuti aonetsetse kuti aliyense akhale wa ukhondo komanso pasapezeke ochita chimbuzi padera. Mr chenya ati nthendayi yabuka kamba kozithandizira mtchire komanso m’bali mwa nyanja zomwe zaipitsa dera lawo. Iwo akupempha boma kuti lichilimike potumiza nthandizo la zaumoyo mwansanga kuti nthendayi igonjetsedwe msanga.
www.avantmalawi.com
DR MWALE