Kondwani Chirwa amene ndi oyimba wa nyimbo za Mulungu watengera Mussa Bwemba ku bungwe la mgwirizano wa oyimba Mmalawi pa nyimbo yotchedwa “kumwamba komweko.”
Izi zachitika pamene Mussa Bwemba amene alinso m’modzi mwa oyimba nyimbo zamatamando (praise team) ku Good News Ministries wakhala akuyimba nyimbo ya Kondwani Chirwa asanamupemphe mwini wake.
Ambiri amene samkayidziwa nyimboyi anayimvera ku Mnsonkhano womwe Kunabwera mtumiki wa Mulungu wochokera ku Zimbabwe a Prophet Walter Magaya ku Lilongwe Golf Club, mwezi watha.
Chinautsa dzaye mchakuti Tchalitchi cha Good news Ministries chomwe chili ku area 47 ku Lilongwe chidayitana a Kondwani Chirwa kudzera mwa a Sam Maliza kuti adzayimbe pa mnsonkhanowo.
Izi zidakanika pazifukwa zimene sizikufotokozedwa bwino ndipo mmalo moti a Chirwa akayimbe nyimboyi a Mussa Bwemba adatsogolera gulu la matandolo (Praise team) ya mpingowo mkuyimba nyimboyi ku mnsonkhanoko mwini wake asadauzidwe.
Mukufotokoza kwa a Kondwani Chirwa akuti iwo sakuletsa munthu kuyimba nyimbo zawo. Koma padali mgwirizano umene sunalemekezedwe pamene a Mussa adayimba nyimboyi.
Ngakhale izi zili chomwechi, anthu ochuluka adali ndi chidwi ndi nkhaniyi chifukwa nyimbo za uzimu za anthu osiyanasiyana zimayimbidwa mmalo opemphera ambiri popanda chifukwa, ngakhale mwini wake asakudziwa.
Zambiri tsatani mu kanema munsimuavantmalawi.com