THE MATTER IS IN COURT
Mlandu wa yemwe anali wachitetezo wa president wakale a wa dziko lino Peter Mthalika a Norman chisale lero unalinso mu bwalo la milandu pomwe mboni za boma zimapitiliza kupereka umboni pa nkhani ya setifiketi yomwe akuti chisale anagwilitsa ntchito.
Avant publications inali nawo ku bwalo la milandu komwe yamvera umboni wonse.
Zikuoneka kuti boma linakonzekera bwino pa mlanduwu pomwe linaitanitsa wankulu owona zolemba anthu ntchito ku MDF kuti azauze bwalo momwe achisale analowera ntchito.
A major General Alick Mhone anauza bwalo kuti mu chaka Cha 1996 pa 6 September ku dedza MDF inalemba ntchito munthu yemwe Zina lake anali Pitious hiwa chisale koma atangolembedwa ntchito dzinali munthuyo anali sintha kukhala paulos chisale zomwe zinadabwitsa anthu ku MDF komabe sizinasinthe chilichonse poti MDF inali kale ndi zikalata zapoyamba zoonetsa pitious hiwa.
Kenaka yemwe anali mkulu wa manebu nthawi ime neyo a chunda nawo anapereka umboni wawo Ku bwaloli ndipo iwo anati mu Chaka Cha 1995 a Pitious hiwa komanso a paulos chisale onse analemba mayeso awo koma a Pitious hiwa anakhoza pomwe a paulos chisale analephera.
Boma silinasiyile pompa koma kuitanisanso wachiwiri kwa mphunzitsi wankulu pa sukulu yomwe awiriwa anaphunzira . Iwo anauza bwalo kuti a paulos chisale analephera mayeso a fomu 2 muchaka Cha 1995 ndipo a Pitious hiwa ndiwo anapambana mayeso.
Boma Lili ndi mboni zisanu ndi ziwiri ndipo latsala ndi mboni zitatu kuti ziperekere umboni wake.
Boma likuwaimba Mulandomu a Norman chisale kuti analowera ntchito setifiketi yakuba yomwe sinali yawo. Iyitu ndi setifiketi ya fomu 2 yomwe malingana ndi bungwe la manebu likuti achisale sanakhoze mayeso awo.
Malingana ndi umboni womwe waperekedwa mu bwalo la milandu zikuonetsa poyera kuti mulanduwu uwavuta a chisale poti kuba setifiketi ndi Mulandu waukulu.
www.avantmalawi.com
DR MWALE