NKHANZA ZIKUPITILIRA KU SECONDARY YA NSANJE

Kuchitira nkhanza ophunzira a folomu 1 pa sukulu ya sekondale ya Nsanje kudakapitilirabe.

Ophunzira a folomu 1 pa sukulu ya sekondale ya Nsanje anali kakasi kusowa pogona usiku wa pa 13 November 2022 kamba koti ophunzira a folomu 4 akumawamenya modesta nkhawa.

Ophunzira oposa 20 omwe tinakumana nawo ati anyamata a folomu 4 wa a kuwamenya pogwiritsa ntchito malamba, ma squeeza ndi zipangizo zina zoopsa,ankangoziyendera kamba koti alibe pogona ndipo ati sakudziwa kuti agwira mtengo wanji.

Iwo anauza mtolankhaniyu kuti aka sikoyamba ponena kuti chibwelereni pasukuluyi ophunzira a folomu 4 wa akuti akhala akusonkhetsa ndalama zoti akatulutsire chimbale cha nyimbo chomwe mpaka pano sikutidziwa kuti nyimbozo anayimba ndi ndani.

Mphunzitsi wa mkulu pasukuluyi, Overton Chikuni nditawayimbira ati tiwapatse nthawi kuti afufuze kuti chachitika ndi chiani kuti zinthu zifike pamenepa.

Izi zikudza pomwe boma adaletsa nkhani zomachitirana nkhanza msukulu za sekondale za mdziko lino.

Tikupatsirani zambiri za nkhaniyi pa avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *