NDONDOMEKO YA AIP YALOWA CHINYENGO KU BILIRA – NTCHEU

Ndondomeko ya kagulidwe ka fetereza otsika mtengo ikupitilira kukumana ndi Mavuto mmadera osiyanasiyana.

Ku Bilira muboma la ntcheu anthu ali kakasasi kamba koti ogulitsa fetereza wotsika mtengoyi pa admarc ya Bilira akufuna k15000 yoonjezera kuti agule fetereza.

Chomwe chikuchitika ndi chakuti fetereza akabwera mafumu ndi abale awo amaitanizana mwanseli ndikukagula fetelezayo pa mtengo ovomerezeka ndi boma koma akangomaliza iwo pamabwera anthu omwe amakhala amkhala pakati omwe akumazatenga ndalama yokwana K15000 kwa ofuna kugula fetelezayu ndipo akatero amakajambulitsa mwachangu ndikugula feteleza. Izi zikuthandauza kuti matumba awiri a feteleza otsika mtengoyi akugulitsidwa pa K45000 ku Bilira ndipo izi zikuchitika ndi ogwira ntchito kumeneko.Avant publication inakayendera malowa mwakachetechete ndipo atafunsidwa anthuwo chomwe chikuchitika anafotokonza kuti “tikusowa mtengo ogwira kamba koti ife tinakonzekera K30,000 pa matumba awiri koma lero tikuuzidwa tipeleke ndalama Ina yoonjezera zomwe ambirife sitingakwanitse ndipo lanthu ndi dandaulo kuti boma lichitepo kanthu kuti anthufe tigule fetereza Malingana ndi mtengo wa boma” anatero mkulu wina yemwe wakana kumutchula dzina. Avant publication inayetsera kuti tilankhulane ndi ogwira ntchito Pamalopo koma anakana

Boma lamalawi likuyenera kusamala kwambiri ndi ndondomeko ya fetereza otsika mtengoyi chifukwa ikukumana ndi zovuta zambiri. Nduna ya za ulimi ikuyenera kutumiza anthu mderali kuti akaone okha zomwe ogulitsa feterezawa akuchita. Ndondomekoyi ndi ya anthu ovutika koma ndizokhumudwitsa kuti ma venda nawo akugula fetereza yemweyu ndikumagulitsa modula.

Pa nkhani ngati yomweyi anthu aku Dedza kwa mfumu yaikulu kasumbu nawo maso akadali kunjira popeza feterezayu sanafikebe mpaka lero zomwe zikuwadetsa nkhawa kuti zikhala bwanji ngati sabwera fetereza?

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *