Akulu akulu omwe akuyang’anira bwalo la Bingu aletsa mneneri sherperd Bushiri kuti asachititse msonkhano wake wa CROSSOVER pa bwalo la Bingu kamba ka zifukwa zawo.
Malingana ndi kalata yomwe Avant publications yaona yati iwo aletsa mpingo wa ECG kamba koti bwaloli lizakhala likuyenderedwa ndi a FIFA kuti azaone ngati lili layenera kuchititsa ma sewero a afcon. Komanso akukamba kuti njira zopewera kachilombo ka covid19 sizizatsatilidwa.
Kodi kamuzu stadium ndi Bingu bwalo losayenera kuchititsa masewero ndi liti? Mesa kamuzu inachitutsa maswero a pakati pa malawi ndi bukina faso? Mmalawi muno afifa kubwera angazasiye bwalo la Bingu kunena kuti ndi losayenera?
Mafunsowa akudabwitsa amalawi ponena kuti akulowetsa ndale pa nkhani ya kagwilitsidwe ka ntchito kabwaloli.
Mmbuyomu tinaona boma la DPP likuletsa a mgwilizano wa Tonse kukachita mwambo wawo pa bwaloli ndipo zinathekadi, Kodi pano tidziti bwaloli akulamulirabe ndi a DPP? Chifukwa zitha kukhala zodabwitsa kuona boma lomwe mtsogoleri wake ndi m’busa kuletsa m’busa mzake kuchititsa msonkhano . Inde tikudziwa kuti mwina izi apangamwaokha oyang’anira bwaloli ndipo president sizikumukhudza Koma funso ndi loti apresident achilandila bwanji?
Malingana ndi amalawi ambiri akuti oyang’anira bwaloli achita izi pofuna kumuchititsa manyazi Bushiri kuti aziti anthu akwawo akumukana pomwe sizili choncho.
Avant publication yati ili likhale phunziro kwa anthu omwe amakondanso kupanga chitukuko kunja nkumaiwala kwawo ndipo adziwe kuti kwa eni ndi mu ntengo tsiku lina uzatsika. Mawu awa apite kwa mtsogoleri wa ECG a Bushiri kuti anakomedwa ndi dziko la south Africa koma osamanga church kwawo kuno, akadakhala kuti ali ndi church si bwezi izi zikuchitika ndipo takhulupilira kuti Ili ndi phunziro kwa mneneri Bushiri. ndipo amanga church chake msanga
www.avantmalawi.com
DR MWALE