MZIMAYI WINA WATAYA MWANA WAKE KU KAWALE

Apolisi ku Kawale mu Mzinda wa Lilongwe akusakasaka mzimayi yemwe sakudziwika yemwe wataya mwana wa ng’ono wa mkazi ku Area 44.

Pa usiku wapa 19 December 2020, mzimayi wina yemwe sakudziwika anataya mwana wa mkazi wa ng’ono kunja kwa nyumba ya mayi Vailet Kasisa a zaka 44.

Mayi Vailet Kasisa pakati pa usiku anamva kulira kwa mwana wa ng’ono kunja kwa nyumba yawo kenako atatuluka panjapo anapeza kuti mwanayo anali atasiyidwa yekha yekha pa njapo.

Apolisi akusakasaka mzimayi yemwe wataya mwanayo.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *