MLANDU WA KU KHOTHI UKOMERA A CHILIMA

THE MATTER IS IN COURT

Mlandu wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulosi Chilima unalowanso mubwalo lero pa 1 August 2023. Achilima anamangidwa ndi bungwe la ACB kamba koti akuganizilidwa kuti analandila ndalama zokwana $280 millions kuchokera kwa a Zanetti sattar.

Lero mmawa achilima anafika kubwalo lamilandu monga mwa ma siku onse. Ndipo posakhalirsa mulandu unayamba. Odandaula omwe ndi a bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu anapempha bwalo kuti awalore akonze kaye Ina mwailandu yomwe a chilima anawamangira. Iwo amati akufuna kuti bwalo limitse kaye mulanduwu kufikira bungweri litakonzekera bwino pa mulanduwu.

Izi sizinasangalatse odandaulidwawa ndipo zinapangitsa a loya a kalekeni kaphale kutsutsa pemphero ndipo mmawu awo a kaphale anati izi sizoloredwa mmalamulo akayendetsedwe ka milandu.pamenepa loya wina wa achilima a khumbo soko anati iwo ndi odabwa kuti bungwe la ACB likufuna kutsintha mfundo Zina pa mulanduwu patadutsa miyezi 9 chimangileni olakwayo. Iwo anati bungweri linali litakonzeka bwino lomwe pomanga achilima choncho likuyenera kupitiliza ndi mfundo zomwezo osasinthanso ayi.

Apa oyimira achilima anapempha bwalo kuti lichonse mfundo zonse za belo zomwe anawapatsa achilima.

Mfundozi zinapangitsa oweruza a redson kapindu kuimitsa kaye mulanduwu mpaka chigawo cha kumadzulo.
Kenako chigawo cha kumadzulo chitafika a kapindu anapereka chigamulo motere. ” mfundo zonse za Belo ya achilina zachotsedwa ndipo iwo ati passport ya achilima isakhalenso mmanja mwa boma koma kuti ikakhale ndi pulezidenti a chakwera chifukwa chakuti a chilima sangatuluke kunja popanda achakwera kudziwa. a kapindu ati a chilima aziziwitsa bungwe la ACB komanso khoti masiku atatu asananyamuke ulendo wawo, iwo anaonjezera kuti uku sikupempha chilolezo koma kungowaziwitsa.
Akafuna kupita kunja azinena tsiku lopitila komanso lobwerera.

Jajiyu wachosanso gawo lomwe limanena kuti achilima azikaonekera ku ACB kamodzi pa miyezi itatu ponena kuti sizikupereka mfundo yeniyeni kwa munthu wa udindo ngati a chilima. Iwo anaonjezera kuti zonsezi zachotsedwa chifukwa achilima si munthu oti angathawe ayi.

Bwalo liika tsiku loti mulanduwu uzayambe kumvedwa koma khoti lati silikhuzidwa ndi zonse zomwe a ACB akuchita pa nkhaniyi.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *