MIGISTRATE NKHONO AWERUZA MOKOMERA A DZIMADZI

Dzina loti dzimadzi silingakhale lachilendo mkamwa mwa amalawi, kamba ka kanema yomwe inatukuka chaka chatha akumenya mwana kamba koti anamubera.

Amabungwe ndi anthu ena omenyera ufulu mothandizana ndi apolisi anachita changu pomanga mkukuyi ndipo abwalo anamukaniza belo mpaka lero.

Koma oweruza justice nkhono wapeza kuti mkuluyi alibe milandu kamba koti sanali ndi cholinga  chofuna kuvulaza mwanayo komanso boma lalephera kupereka umboni okwana kuti adzimadzi amafuna kuvulaza mwanayo.

Chigamulochi chikuthandauza kuti mkulu siolakwa ndipo amuuza kuti alibe mlandu, tikunena pano watuluka.  Komatu amalawi ambiri sanailandire bwino nkhaniyi ndipo akudabwa kuti oweruza waganiza bwanji potengera ndi kanema yomwe amalawi anaona yomuchitira nkhanza mwanayu.

Anthu ena omwe avant publications yayankhula nawo kuntcheu ati ndi odabwa kumva kuti mkuluyi siolakwa komanso kuti nkhaza zimagawidwa mmagulu ofuna kuvulaza komanso osafuna kuvulaza munthu.

Monga inuyo amalawi malingana ndi mmene munaonera kanema ameneyu komanso potengera chigamulo cha a magistrate nkhono nkhaniyi yaweluzidwa bwanji? Maganizo anu.

www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *