Amalawi ndi okwiya kamba ka malankhulidwe a nduna yoona za magetsi a Ibrahim matola omwe alankhula monyoza kuti amalawi omwe akudandaula zoti mtsogoleri wa dziko lino akuyenda kwambiri ndi achule. Ndipo iwo ati ndunayi ipepese ndipo a chakwera achitepo kanthu.
Lolemba president chakwera amatsekulira mphamvu ya magetsi yokwana 20 mega wats yomwe ikuchokera ku mphamvu ya dzuwa yomwe yakhazikitsidwa mu boma la Dedza. Kumeneku nduna ya zamagetsiyi inayamikira a president pokwanilitsa malonjezo awo owonetsetsa kuti magetsi asamathimeme mdziko muno. Koma kuyamikira kuli apo ndunayi inaulukitsa nkuphonya chitsa pomwe inalankhula mmaso muli gwa kuti apresident musawamvere achulewa omwe alulankhula kuti musamayendende ndicholinga choti muteteze chuma cha dziko lino. Inuyo a president yendani ndipo gwirani ntchito yanu momasuka.
Sabata yatha president chakwera anachititsa msonkhano wa atolankhani ndipo mmawu ake iye anakhazikitsa mfundo khumi ndi zisanu zomwe mwaimodzi ndi yoti iye ndi. Nduna zake komanso anthu ena ogwira ntchito mu boma asamayendende. Mfundoyi inasangalatasa amalawi poganiza kuti mtsogoleriyu wamva madandu awo, komatu izi sizinali chomwechi mmalingaliro a nduna yoona za mphamvu za magetsiyi popeza iwo awuza mtsogoleriyu kuti asamavere zomena za anthu ndikumayenda mmene angafunire. Akanangonena mwa njira ina sibwezi zitavuta koma amatola anyogodola ponena kuti omwe akudandaulawo ndi achule. Ndipo izi zakwiyitsa amalawi omwe akuti mkuluyi apepese.
Amalawi ambiri ndi okhumudwa ndi malankhulidwe a a Matola ponena kuti mu chaka cha 2020 iwo analankhulanso monyoza mtsogoleri wa bungwe la MEC panthawiyo a Jane ansa ponena kuti achoke pa mpando mwachangu ngati zikuvuta atha kuwathandiza kulongeza ma kamisolo komanso ma panti awo kuti achoke mwa changu. Angakhala Jane ansah analakwira mtundu wa amalawi kuphatikizapo a Joyce banda, mtsogoleri wa chipani cha PP sanasekere koma kuzuzula amatola za malankhulidwe awo onyozetsa azimayi. Lero ndi izi amatola akupitilizabe malankhulidwe awo osasamala mpaka kunyoza gulu la amalawi ochuluka omwe anaika achakwera pa mpando mu 2020 kuti iwo akhale nduna lero kuti ndi achule.
Ndi achule omwewa amapanga ma demo kuyambira 2019, kuti amatola akhale nduna lero.ndi achule omwe anali pa msonkhano ku dedza komwe komwe ndunayi imawalankhula ndi achule omwe anavotera chakwera ameneyu kuti amatola akhale nduna ndipo ndi achule omwewa omwe akufuna azavotere chakwera mu 2025 kuti amatola azakhalebe nduna. Kodi achakwera ndi chipani cha MCP mwailandila bwanji nkhaniyi?
Posachedwapa taona mlembi wa president a zangazanga chikhosi atachotsedwa pa udindo wawo . Izitu sizinangochutika koma kuti amalawi amadandaula ndipo mtsogoleriyu anamva. Amalawi (achule) akudikira kuti amve zomwe zichitike pa nkhaniyi.
www.avantmalawi.com
DR MWALE